• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-15] Mungalandire Mzimu Woyera Ndi Kukhala Naye Pokhapo Ngati Mwadziwa Choonadi (Yohane 8:31-36)

Mungalandire Mzimu Woyera Ndi Kukhala Naye Pokhapo Ngati Mwadziwa Choonadi(Yohane 8:31-36)
“Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m’mau anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani. Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji, Mudzayesedwa aufulu? Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, Indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo. Koma kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse. Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.”
 

Kodi tiyenera kuchita chiani kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera?
Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kukhala  mwa chikhulupiliro.

Kodi mudziwa kuti choonadi ndi chiani? Yesu anati, “Ine ndine coonadi” (Yohane 14:6). Choncho kudziwa Yesu ndi kudziwa choonadi. Kodi Mzimu Woyera omwe umakhala mwa inu umathokoza chikhulupiliro chanu mu uthenga wabwino okoma? Muyenera kuzindikira kuti ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi chiyeretso chaumunthu cha uthenga wabwino okoma ndi kukhulupilira mwa iwo. 
Anthu masiku ano nthawi zonse amagwiritsa ntchito kafotokozedwe ka ‘kubadwa mwatsopano.’ “Anthu ayenera kubadwa mwatsopano. Ndale ziyenera kubadwa mwatsopano. Chipembedzo chiyenera kubadwa mwatsopano.” Amagwiritsa ntchito mawu amenewa ngati njira yopita ‘patsogolo.’ Koma, kubadwa mwatsopano sikutanthauza kupita patsogolo mu mkhalidwe la thupi. Kubadwa mwatsopano kukutanthauza kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwa kumvetsera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
 
 

Kodi ndi mawu otani a choonadi amene amatilola ife kuti tibadwe mwatsopano?


Kodi ndi chifukwa chiani munthu ayenera kubadwa mwatsopano? Munthu siwathunthu, choncho ayenera kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuti abadwe mwatsopano ngati mwana wa Mulungu. Tingaone anthu ambiri amene amakhulupilira mwa Yesu koma alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Nikodemo anali olamulira wa Ayuda. Nikodemo amene amaonekera pa mutu 3 wa Yohane, anali mtsogoleri wa Ayuda amene anayesa kusunga lamulo limene linaperekedwa ndi Mulungu. Koma, anali kugwira ntchito ngati mtsogoleri wa chipembezo wa anthu. Osadziwa za kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kukhala mwa chikhulupiliro. Munthu angalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhapo pamene wayamba kukhulupilira mu mawu a choonadi mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Yesu anati, “Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?” (Yohane 3:12)
Uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi otere. Ambuye wathu anabadwira m’dziko lino, anabatizidwa ndi Yohane ali ndi zaka 30, anafa pa Mtanda patatha zaka zitatu, anaukitsidwa ndipo motero anatiombola ku machimo onse. Anakhala Mpulumutsi wa iwo amene akhulupilira kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane ndi kuuka kwa akufa. Anapereka chikhululukiro cha machimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. 
Iwo amene adakali ndi uchimo m’mitima mwawo ayenera kukhululukidwa machimo awo pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Munthu sangaleke kuchita machimo pamaso pa Mulungu ndipo choncho ayenera kupulumutsidwa polola Yesu ngati Mpulumutsi wake. Yesu anatsuka machimo onse a dziko ndi uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Ochimwa onse angapulumutsidwe mwa kumvetsera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndi odalitsidwa ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
“Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa” (yohane 3:14). Mu Chipangano Chakale, ngakhale kuti anthu a ku Israyeli anali kuchita machimo, analumidwa ndi njoka yamoto m’chipululu, ndipo anali kufa mwachisoni, ambiri anakwanitsa kukhala poyang’ana njoka yamkuwa imene inaikidwa pabwino. 
Chimodzimodzi, tiri ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Yesu amapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Satana amatitsekereza ife kuti tisadziwe uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndipo amayesa kutitchinga ife kuti tisalandire Mzimu wa choonadi. Komabe, Mulungu anatidalitsa ife ndi chikhululukiro cha machimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mwa chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. 
Mungalandirenso kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngati mwakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu. Kodi m’madziwa uthenga wabwino okoma umenewu ngati choona pamaso pa Mulungu? Kodi mumakhulupilira kuti mumatha kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mwa umenewu, uthenga wabwino oona? 
Ambuye anatiuza kuti tidziwe choonadi chimene chimatipulumutsa ku machimo athu onse. “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32). Kodi mukudziwa choonadi cha uthenga wabwino okoma chimene chimatipulumutsa ife ndi kutidalitsa ife ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera? Ngati mudzalola uthenga wabwino okoma umenewu, ndiye kuti muzalandiradi kukhazikika kwa Mzimu Woyera.