• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-16] Ntchito ya Onse Amene Alandira Mzimu Woyera (Yesaya 61:1-11)

Ntchito ya Onse Amene Alandira Mzimu Woyera(Yesaya 61:1-11)
“Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzodza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; ndikalalikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro m’Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m’malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m’malo mwa maliro, cobvala ca matamando m’malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe. Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri. Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa. Koma inu mudzachedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu muzadya cuma ca mitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao. M’malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi citonzi iwo adzakondwera ndi gawo lao; cifukwa cace iwo adzakhala naco m’dziko mwao colowa cowirikiza, adzakhala naco cikondwerero cosatha. Pakuti Ine Yehova ndikonda ciweruziro, ndida cifwamba ndi coipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m’zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha. Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa. Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandibveka ine zobvala za cipulumutso, nandipfunda copfunda ca cilungamo, monga mkwati abvala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zace, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa cilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.”
 

Kodi ntchito ya amene alandira Mzimu Woyera ndi yotani?
Ndi kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa anthu onse a dziko lapansi.

Kodi munthu amene walandira Mzimu Woyera ayenera kuchita chiani? Ayenera kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa anthu onse. Mulungu anapereka uthenga wabwino okoma wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu kwa iwo amene analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera Iwo amene anakhululukidwa ku machimo awo pamaso pa Mulungu analandira Mzimu Woyera. Nanga kodi mukuganiza kuti ndi chifukwa chiani Mulungu anapereka mphatso ya Mzimu Woyera kwa Iwo? 
Kuti awapatse chitsimikizo chomaliza kuti wapanga iwo kuti akhale ana Ake, anawapatsa mphatso ya Mzimu Woyera. Iye amawapatsanso mafuno abwino owathandiza kugonjetsa Satana. Amapanga iwo amene anakhululukidwa machimo awo ndipo analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuti achite zotsatira: 
 
 

Amawapanga iwo kuti alalikire uthenga wabwino kwa osauka 


Kodi nkhani yabwino kwa osauka ndi yotani? Ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mulungu analamula iwo amene analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuti alalikire uthenga wabwino okoma kwa osauka. Iwo amene analandira Mzimu Woyera, popeza ali ndi chiyembekezo cha Kumwamba, sakhutitsidwa ndi zinthu pa dziko lapansi. 
Mulungu anapereka uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa osauka ndi kuwakhululukira machimo awo. Iye kenako anapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo ndi kuwalola iwo kulowa m’dziko la muyaya. Mulungu analamula olungama kuti alalikire uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa osauka. Anawauzanso kuti afalitse chikhulupiliro mwa Mulungu ndi Yesu. Chifukwa chimene Mulungu anatipatsa Mzimu Woyera chinali chakuti tilalikire nkhani yokoma mochuruka kwa osauka a dziko lapansi. 
 
 

Amatituma ife kuti tichiritse a mtima osweka 


Kodi Ambuye wathu amachiritsa motani maganizo athu? Amachiritsa mtima osweka ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kuli anthu ambiri ali ndi mitima yosweka. Kwa iwo, moyo ndi opanda ntchito, ndipo chilungamo chawo ndi chosweka. Ali ndi miyoyo yodzichepetsa ndiponso yowawa chifuwa cha machimo awo. Motero, nthawi zonse amazunzidwa ndi kukaikira kwawo za moyo. Anthu onse amafuna kukhala mwachisomo ndipo amafuna kusangalala kuchita bwino kwao mu thupi ndiponso moyo wawo, koma ichi sichimachitika mosavuta mwa njira imodzimodzi ngati pamene anthu abeledwa katundu wawo ndi akuba. 
Chimodzimodzi, iwo amene ali ndi uchimo mu mtima mwawo akubeledwa nthawi zonse chilungamo chawo chonse, ndipo pothera pake, amapita ku gehena chifukwa cha machimo awo. Ndi chifukwa chake Ambuye, pakumvera chisoni mitima yawo yosweka, analamula ife kuti tilalikire uthenga wabwino okoma kwa iwo. Kodi Mulungu anawachiritsa iwo ndi mawu otani? Anachita choncho ndi uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Anawachiritsa amtima osweka ndiponso kuwapatsa iwo moyo osatha. 
 
 

Amanenera zaufulu kwa akapolo a uchimo 


Iye amapereke ufulu kwa akapolo. Kodi ichi chikutanthauza chiani? Chikutanthauza kuti Mulungu wamasula miyoyo ya anthu ku machimo onse a dziko. Iye wapereka cholinga chimenechi kwa okhawo amene analandira Mzimu Woyera, ndipo angamasule ena ku machimo awo. 
Munthu ali ndi thupi ndiponso moyo. Ndipo thupi lake ndi moyo wake zilipo, zomangidwa ndi temberero la uchimo ndiponso lamulo. Sangachite chirichonse koma kukhala monga kapolo wauchimo, mosasamala kanthu kuti mwina amakhulupilira mwa Mulungu kapena ai. Pobadwa ndi uchimo, sangazithandize koma kuchimwa. Motero, ndi oyenera kukhala ngati kapolo wa uchimo pa moyo wake onse. Amakhala mwa njira imeneyi ndipo ndi oyenera kuonongedwa pamapeto. 
Ndi chifukwa chake amakhala ndi moyo osapeweka pamene akuchita zinthu zozimvetsa chisoni kupatura kufoka kwake kumene kwamuika mu mkhalidwe umenewu. Mulungu anatumiza Mzimu Woyera kwa iwo amene sangathe koma kuchimwa ndipo ndi oyenera kufa, kotero kuti alalikire uthenga wabwino okoma kwa akaidi auchimo, ndi kupatsa akapolo ufulu ku uchimo wawo onse. 
 

Amatonthoza onse amene amalira 
 
Kodi Mulungu anapereka chiani kwa iwo amene amalira? Powapatsa iwo uthenga wabwino wa chikhululukiro, Mulungu amatonthoza anthu onse a dziko lapansi amene amalira. Anatuma Yesu Kristu m’dziko lino kuti akhululukire mtundu wa anthu ku machimo awo. Ndi kupereka machimo onse a dziko pa Iye, anapangitsa Iye kuti abatizidwe ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda. Umu ndi m‘mene Mulungu anayeretsera ife ku machimo athu. Motero, Mulungu anapulumutsa ife ku machimo onse a dziko lapansi. 
Ambuye wathu amatonthoza onse amene amalira mwa kuwadziwitsa za uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Mwa kuchita choncho, amadalitsa iwo amene akuvutika ku chikhulupiliro chochepa. Amatsogolera iwo okha amene ali ndi Mzimu Woyera kuti alalikire uthenga wabwino umenewu, kuti achiritse a mtima osweka ndi kumasula akapolo ku uchimo. 
Cholinga cha kupezeka kwathu m’dziko lino ndi chakuti tikhululukidwe ndi Ambuye wathu ndipo kenako tilalikire uthenga wabwino okoma kwa iwo amene ndi omangidwa ndi uchimo ndipo akufuna chitonthozo kuti amasuke ku uchimo. Mulungu amatiuza kuti ngakhale kuti miyoyo yathu ndi yaifupi, sikuti ilibe ntchito konse. Kuti Mulungu anakonzekera chikhululukiro chathu ndi madalitso abwino kwambiri a mtundu wa anthu ndi chizindikiro cha choona chimenechi. 
Ambuye wathu anapereka korona wa ulemerero kwa onse amene amalira. Ichi chikutanthauza kuti ochimwa akhululukidwa ku machimo awo zikomo ku ubatizo wa Yesu ndipo motero tingalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Ngati munthu wakhululukidwa ku machimo ake, maganizo ake amatsitsimuka ndipo amayamika madalitso abwino amenewa. Ambuye wathu amamuveka iye korona wa ulemelero. Iye anapatsa ochimwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kupanga iwo amene akhulupilira m’menemo ana Ake. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu amapangidwa kukhala ndi chimwemwe m’malo mwa kukwiya. 
Monga momwe anthu onse amabadwa ndi kufa ndi kulira, chimwemwe ndi chosakhalitsa, ndipo maganizo awo ndi odzala ndi mkwiyo. Komabe, Mulungu anakumana nawo ndipo anawapangitsa kuti abadwe mwatsopano ndi chiyembekezo komanso chisangalalo. Chimodzimodzi, iwo amene ndi obadwa mwatsopano pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma amakhala ndi moyo watsopano ndiponso ali ndi ntchito yatsopano. Kuonjezerapo, amatha kuchita zimene Mulungu akufuna, chimene ndi kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ku ochimwa onse a kudziko, kuchotsa nkwiyo onse m’mitima yawo ndi kuwalola iwo asangalale ndi khalidwe lonse la chimwemwe ndi kukondwa m’malomwake. 
Iwo amene akhululukidwa machimo awo ndi Mulungu amapereka ulemerero kwa Iye. Anauza olungama kuti alalikire uthenga wabwino okoma. Anawauza iwo kuti alalikire m’mene Iye alili, uthenga wabwino umene anatipatsa ife, ndiponso m’mene ulili ulemelero wa Ufumu wa Kumwamba umene anatikonzera ife. Tingaone ulemerero wa Mulungu mwa iwo amene anakhululukidwa ndi Iye . Iwo amene anali kulira mu moyo wawo asanadzadzidwe ndi Mzimu Woyera tsopano akukondwa m’chimwemwe, iwo amene anali omangidwa mu uchimo tsopano akumva kukondwa mu ufulu, ndipo iwo amene anali ndi moyo opanda ntchito tsopano akukhala ndi moyo olungama. Awa onse akuonetsa ulemelero wa Mulungu. Mulungu anatchula olungama monga iwo amene adzamanganso choonongedwa chakale, kuukitsa zopasuka zakale, ndi kukonzanso mizinda yowonongedwa. 
Zoona zake, uthenga wabwino okoma umenewu wa madzi ndi Mzimu unali uthenga wabwino olalikiridwa ndi Atumwi m’masiku a mpingo oyambirira. Yesu anatumidwa dziko lapansi papfupifupi zaka zikwi ziwiri zapitazo. Uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu wakhala ukulalikidwa m’dziko lino kufikira AD 300. Uthenga wabwino olalikiridwa ndi olungama masiku ano ndi uthenga wabwino umodzimodzi wa Mzimu Woyera, umene Atumwi analalikira pa nthawi imeneyo. Komabe, m’masiku a m’zaka zoyamba za mazana anayi za Mfumu ya ku Roma pamene Roma anapanga Chikristu kukhala chipembezo cha dziko ndi kupereka kwa mzika zake ufulu wa chipembedzo, uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu unachotsedwa ndipo unasowa pang’ono pang’ono. Ndi pambuyo pa chimenechi, pamene Chikristu monga chipembezo chokhazikitsidwa chinakhala chodziwika kwambiri, moti anthu amodzimodzi amene ankalalikira uthenga wabwino oona anasowa. 
Kodi ndi chifukwa chiani chikhulupiliro cha iwo amene anakhulupilira ndi kulalikira Chikristu choona ndi uthenga wabwino oona chinasintha? Pamene Chikristu chinakhala dziko la chipembezo la Ufumu wa Aroma, Akristu anakhala ndi ufulu mu zinthu zambiri zoletsedwa ndipo anasangalala ndi ufulu umodzi monga nzika za Roma. Akristu ndiyeno anatha kukwatira ngwazi za chi Roma, ndipo anali kulowa mu ntchito za boma. Chifukwa cha ufulu umenewu, chikhulupiliro chawo chinachepa kuchoka ku chikhulupiliro cha kuukitsidwa kupita ku chipembezo chawamba. Kuchokera pamenepo, uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu unaleka kuoneka, ndipo mbiri yochepa ya Chikristu inayamba kukula. 
Mulungu amalamula ife Akristu omaliza pa nthawi Yake yakudza modziwikiratu kuti tikalalikire uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu umene unaponyedwa kuti uonongedwe kwa nthawi yaitali yotere, ndipo motero upulumutse anthu ku machimo awo. Adzabwezeretsa uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu umene unalalikidwa m’masiku a Atumwi. Uthenga wabwino m’masiku a Atumwi unali uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Amaticha ife anthu amene timakonza mzinda oonongedwa. Anatipanga kuti tiphunzire ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndi kutipanga alimi a munda Wake wa mphesa. 
Mulungu anatipatsa ntchito yomweyi monga anachitira kudzera mwa Atumwi. Anapanga inu ndi ine kuti tilalikire uthenga wabwino weniweni wa madzi ndi Mzimu. “Mzimu wa AMBUYE Yehova uli pa ine; pakuti YEHOVA wandidzodza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa” Mulungu anapanga iwo amene analandira kale Mzimu Woyera kuti alalikire uthenga wabwino ndi kutipatsa ife Mzimu Woyera. 
Mulungu anativeka ife ndi korona wa maluwa, kuchotsa kukwiya konse, ndi kutiveka chovala cha matamando pa ife mwa kuika chimwemwe mwa ife. Iwo amene ali ndi Mzimu Woyera m’mitima yawo amabyala mbewu ya uthenga wabwino okoma umenewu kuti ena amlandire Iye. Ndiyeno azalolanso uthenga wabwino opatsidwa ndi Ambuye wathu, adzakhululukidwa, ndipo pomaliza adzalandira Mzimu Woyera. 
Takhala antchito a Mulungu, Inu ndi ine tadalitsidwa ndi ulemelero wa Ufumu wa Kumwamba. Komabe, Mulungu anapanga iwo amene alibe Mzimu Woyera kukhala akhungu kotero kuti asadziwe, asaone, kapena asamvetsetse uthenga wabwino okoma umenewu. Mwina angapangitse ena kukhulupilira mwa Yesu mwa dzina chabe, koma osawapanga kuti alandire Mzimu Woyera. 
Ambuye wachita zinthu zotsatirazi kudzera mwa iwo amene ali ndi Mzimu Woyera. Anawapanga iwo kuti alalikire nkhani yokoma kwa osauka ndi kuchiritsa a mtima osweka ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ndipo anaonetsanso akapolo auchimo ufulu oona wa chipulumutso ndi kutsitsimula onse amene akulira ndi uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Amamasula iwo amene ali omangidwa ndi uchimo chifukwa cha kufoka kwawo, kuwapatsa iwo chimwemwe ndi chiyembekezo ndipo kenako anakwera Kumwamba. 
Potsatira zimenezi, Mzimu Woyera umene umakhala mwa ife unatipanga ife kuti tilalikire uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa anthu onse. Yesu Kristu anauza iwo amene akhululukidwa ndipo ali ndi Mzimu Woyera mwa iwo kuti apulumutse ochimwa onse ku machimo awo. Ambuye anapatsa mphamvu iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuti alamulire zimene Iye anakonza kuti achite. Anapanga anthu olungama onse kuti achite ntchito Yake. Ife ndife antchito Ake, amene tinasankhidwa ngati oyang’anira munda Wake wa mphesa, mpingo wa Mulungu. Ife ndife akapolo Ake. Mulungu watipatsa ife madalitso odabwitsa amenewa. 
Timazindikira kufoka kwathu tikaona pa thupi lathu, koma popeza Mulungu akugwira ntchito ndi ife, timakhulupilira mwa Iye ndipo takhala atumiki Ake mwa chikhulupiliro. Tikhulupilira kuti Mulungu azachita ntchito zambiri zazikulu kudzera mwa ife ndipo azafalitsa ulamuliro Wake pa ife. 
Mulungu anaganiza za kumanganso zinthu zosiidwa za uthenga wabwino mu mizinda yowonongedwa. Iye analonjeza kuti adzaukitsa zopasuka zakale ndi kukonza mizinda yowonongedwa. Ndikhulupilira kuti kuzakhala kukonzanso kwa uthenga wabwino padziko lonse!
Ichi komabe si chifuniro changa. Ndikuchikhulupilira chifukwa Mulungu ananena kuti zidzakhala choncho. Mbuye wathu anapanga iwo amene ali ndi Mzimu Woyera kulalikira uthenga okoma umenewu padziko lonse lapansi. Iye anatuma Mwana Wake m’dziko lino ndi kukwaniritsa uthenga wabwino, ndipo ndikukhulupilira kuti akukwaniritsanso chifuniro chake kudzera mwa ena a ife amene tiri ndi Mzimu Woyera. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu adzaona ulemelero wa Mulungu. Aleluya!