(Aroma 8:16-25)“Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye: pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilindira bvumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti colengedwaco cagonjetsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca Iye amene anacigonjetsa, ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wacibvundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano. Ndipo sicotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m’kati mwathu, ndi kulindilira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu. Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani cimene acipenya? Koma ngati tiyembekezera cimene siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.”
Tsopano ndi nthawi yopanda chiyembekezo
Kodi n’chifukwa chiani olungama ali ndi chiyembekezo mu Mzimu Woyera?
Chifukwa ife Akristu obadwa mwtsopano tidzakhala ndi kumwamba ndi dziko latsopano ngakhale kuti iwo amene sanabadwe mwatsopano adzanongedwa pamodzi ndi kugwa kwa dziko lino.
Kodi muli chiyembekezo chenicheni tsopano m’dziko lapansi? Ai, mulibe. Chikupezeka mwa Yesu yekha. Tsopano ndi nthawi yosadziwika ndiponso yopanda chiyembekezo. Zinthu zonse zimasintha masiku onse ndiponso mwamsanga, ndipo anthu akuyesesa kwambiri kupitiriza ndi zosintha mwamsanga zimenezi. Iwo safunafuna choonadi chauzimu kapena kudera nkhawa za chisangalalo cha uzimu. M’malo mwake amavutika pofuna kupewa kulephera ndipo amakhala ngati akapolo adziko lino.
Ntchito zatsopano zimaonekera ndipo ntchito zakale zimafa. Chimodzimodzi, anthu akupita mu msintho wodabwitsa. Motero amakhala otanganidwa komanso miyoyo yamantha. Ndipo pang’onopang’ono, chiyembekezo chawo ku dziko lino chimatha. Chimodzi mwa chifukwa chimenechi ndi chakuti akukhala miyoyo yopanda chilimbikitso chirichonse cha mtsogolo. Tikukhala m’dziko losakhazikika chotere.
Tiyenera kuyembekezera Moyo osatha mu Mzimu Woyera
Kodi chiyembekezo chenicheni tingachipeze motani? Tingachipeze icho pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Chiyembekezo cha iwo amene analandira Mzimu Woyera sichili padziko lapansi, koma Kumwamba. Mtumwi Paulo analankhula za chiyembekezo choona cha Kumwamba. Ife amene tinalandira kale kukhazikika kwa Mzimu Woyera timayembekezera zinthu zakumwamba. Timachita choncho chifukwa timakhulupilira kuti Yesu Kristu anabwera kudzachotsa machimo athu onse ndi kupulumutsa ife ochimwa kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane komanso mwazi Wake wa pa Mtanda. Ambuye anapereka chiyembekezo chakumwamba kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa chikhululukiro cha uchimo.
Aroma 8:19-21 anena kuti, “Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilindira bvumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti colengedwaco cagonjetsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca Iye amene anacigonjetsa, ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wacibvundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Zolengedwa zonse zikuyembekezera kuomboledwa ku ukapolo wa chibvundi ndiponso imfa.
Zinthu zonse m’dziko lino sizangwiro, choncho zimafuula ndi kuyembekezera ana a Mulungu kuti avumbulutsidwe. Kuonjezerapo, amafunanso kumasulidwa ku ukapolo wa chibvundi ndi kukhala kwamuyaya. Zolengedwa zonse zimayembekeza tsiku limene sidzidzaola kapena kunyala koma m’malo mwake kukhala kwamuyaya.
Tsiku lina zolengedwe zonse zopangidwa ndi Mulungu zizakonzedwanso mwatsopano. Ngakhale kuti maluwa amanyala ndi kuola m’dziko lino, nthawi zonse adzaphukira ndi kukhala kwamuyaya m’dziko latsopano. Ife amene tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera tizaonanso dziko latsopanoli.
Yesu analonjeza kuti adzabweranso, kuzaukitsa iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, kuwapatsa thupi latsopano limene ndi losabvunda komanso losafa kwa aliyense wa iwo, ndi kuwapatsa iwo moyo osatha. Iye anawalonjezanso kuti adzakhala kwamuyaya Kumwamba pamodzi ndi Mulungu. Zolengedwa zonse m’dziko lapansi zikuyembekezera tsiku limenelo. Izo zidzakhalanso kwamuyaya pamodzi nafe, ana a Mulungu, pamene tsiku limenero lidzafika.
Dziko lino limaoneka kudzera m’chiyembekezo
Kodi ndi liti pamene maloto amenewa amakhala oona kwa olungama? Adzakhala oona pamene Ambuye wathu adzabwera. Tiyenera kukhala mu chiyembekezo pamene tikuyang’ana dziko lino. Yesu ananena kuti kuzakhala njala, milili, zivomerezi ndi nkhondo m’malo osiyanasiyana. (Mateyu 24:7). Koma chimaliziro sichinafike. Pa tsiku lomaliza la dziko lino, Ambuye wathu adzabweranso, kukonza zinthu zonse za dziko ndi kupereka thupi lauzimu losafa kwa ife. Ichi chikutanthauza kuti zomera ndi nyama zizalandiranso matupi osafa. Pokukhulupilira chimenechi, tiyenera kuona dziko lapansi ndi chiyembekezo chatsopano.
M’dziko lino, ngakhale iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera akubuula mkati mwawo pamodzi ndi zolengedwa zonse, mofunitsitsa akuyembekeza ulemerero wa chiombolo cha matupi awo monga ana Ake. Timaona dziko lapansi ndi chiyembekezo chifukwa Ambuye adzatipanga kukhala ana Ake, amene sitizaola konse kapena kufa pamene adzabweranso.
Ngakhale kuti dziko lizaonongedwa tsiku lina, zinthu zonse zizakhala zatsopano pamene Ambuye adzabwerenso. Tiyenera kukhala ndi chiyembekezo pokhulupilira zimenezo. Dziko latsopano lizakhala lachimwemwe ndiponso lodabwitsa monga dziko lina lililonse labwino munawerenga mu mabuku a nthano. Ganizirani za kukhala m’dziko lotere kwa zaka chikwi. Ndipo tizakhalanso ndi moyo osatha ngati ana Ake pamene tizalowa mu Ufumu wa Kumwamba. Tiyenera kukhala ndi chiyembekezo chotere.
Kodi m’maona chiyembekezo chirichonse m’dziko lino? Ai. Anthu amakhala okondwa mu njira yachisangalalo, chifukwa alibe chiyembekezo cha dziko lino. Koma Ambuye wathu wapatsa chiyembekezo cha Kumwamba kwa iwo amene anakhululukidwa ndi kukhala olungama. “Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani cimene acipenya? Koma ngati tiyembekezera cimene siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.” Ichi chikutanthauza kuti tiyenera kukhala opirira mokwanira kuti tiyembekeze kubweranso kwa Yesu chifukwa tinapulumutsidwa ndi chikhulupiliro chathu mu mawu a Mulungu.
Tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera m’moyo wathu chifukwa tinapulumutsidwa ku machimo athu. Ndiko kunena kuti, iwo amene anakhululukidwa mwa Yesu ali ndi Mzimu Woyera m’mitima yawo m’malo mwa uchimo. Nanga bwanji za matupi athu? Matupi athu ofoka adzaukitsidwanso, adzalandira moyo watsopano ndi osafa. Tizakhala kwamuyaya pamodzi ndi Mulungu pamene Yesu adzabweranso. Okhawo amene abadwa mwatsopano ali oyenera kuchita zimenezo mwa chiyembekezo, ndipo motero mzimu wathu ndi thupi zizakhala zangwiro. Thupi lathu lizakhala losatha ndipo sitizakhala odwala. Matupi athu a dziko lapansi ndi ofoka, motero, ndi kosatheka kwa ife kukhala ndi moyo wangwiro. Koma kenako tizakhala ndi moyo wangwiro. Tiyeni tione kutsogolo kwa Kubweranso Kachiwiri kwa Ambuye wathu. Okhawo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera angakhale komanso chiyembekezo ndi moyo otere.
Chiyembekezo cha olungama sichili Kumwamba kokha koma chimachitikanso m’dziko lino. Baibulo limanena kuti Ambuye wathu adzabweranso pamene dziko lino lidzagwa chitatha Chisautso Chachikulu. Iye azabweradi. Pamene anabwera kwa nthawi yoyamba, anabatizidwa chifukwa cha ochimwa, anafa pa Mtanda kuti akhale olungama, ndipo pomaliza anakwera Kumwamba. Tsopano ndi nthawi pamene Ambuye ali pafupi kubweranso.
Pa nthawi imeneyo, adzautsa oyera mtima onse akugona amene anakhulupilira mwa Yesu ndipo analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndipo adzawamasula ku zopinga zachinyengo. Adzawapatsa matupi akumwamba atsopano amene samaola kapena kukhala odwala. Kuonjezerapo, adzatengedwa m’mitambo kukamana Naye mu mphepo ndipo Iye adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.
Kuchoka apo, ife, pamodzi ndi Yesu Ambuye wathu, tizakhala ndi kulamulira pamodzi ndi Iye m’dziko latsopano kwa zaka chikwi mwa malipiro a kutumikira uthenga wabwino. Ichi ndi chikonzekero cha iwo amene akufuna kupita ku Kumwamba. Ichi ndi chiyembekezo cha Kumwamba ndiponso zenizeni. Pa nthawi imeneyo, zinthu zonse zopanda ungwiro zizakhala zangwiro, ndipo zinthu zimene zinayenera kuola sizidzaolanso. Mawu akuti “Lifesedwa m’cibvundi, liukitsidwa m’cisabvundi” (1 Akorinto 15:42), adzakwaniritsidwa pa nthawi yake kudzera mwa Yesu Kristu.
Tiyeni ife amene tiri ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera tikhale ndi chiyembekezo! Muyenera kukumbukira kuti ngakhale zinthu zonse zimafoka ndi kufa, ichi sindiye kutha kwake. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro cha chiyembekezo kuti Ambuye wathu adzapanga dziko lonse kukhalanso latsopano. Tiyenera kukhala mu chiyembekezo cha kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano. Pokhala ndi chiyembekezo chotere, tizatha kulalikira uthenga wabwino okoma.
Tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa tinapulumutsidwa ku machimo a dziko lapansi. Chimodzimodzi, Mzimu Woyera mkati mwathu ukuyang’ana kutsogolo kwa kubweranso kwa Ambuye. Iye amapembedzera kwa Mulungu Atate m’malo mwathu kuti tikhale ndi chiyembekezo komanso chikhulupiliro kopanda kukhumudwitsa mitima yathu.
Tiyenera kukhala m’chiyembekezo mu Mzimu Woyera
Kodi malo olungama ali kuti? Adzakhala mu [5]zaka chikwi momwe Ambuye adzamanganso dziko lino pamene adzabweranso ndi Ufumu wa Kumwamba. Motero, tiyenera kukhala opirira mokwanira kuyembekeza Tsiku limenelo kuti libwere. Tiyenera kukhulupilira kuti Ambuye wathu adzapanga matupi athu kukhala angwiro pamene dziko lino lagwa. Tiyenera kukhala ndi chiyembekezo mu ulemelero wa mawa.
5Pamene Ambuye Yesu adzabwerenso kachiwiri pa dziko lino mogwirizana ndi lonjezo Lake, adzatsika kuchokera Kumwamba, ndi kuukitsa akufa mwa Kristu choyamba. Patatha chimenechi, adzasintha oyera mtima onse, amoyo ndi oukitsidwa, kukhala m’matupi amuyaya osasokonezeka ndiponso osasinthika, ndipo adzapititsa oyera onse m’mitambo kuti akumane ndi Ambuye mu mphepo (1 Atesalonika 4:16-17, 1 Akorinto 15:51-53). Ndiyeno azapanga zinthu zonse zatsopano ataponya mbali zisanu ndi ziwiri za mkwiyo Wake pa ochimwa omwe adzasale. Iye adzakhazikitsa Ufumu Wake pa dziko latsopano, ndipo adzalamulira kwa zaka chikwi ndi iwo amene azatengamo mbali mu kuuka koyamba (Chivumbuluso 20:4-5). Zaka chikwi zitatha, adzaweruza akufa onse, ndi kuwaponya mu ng’anjo yamoto (Chivumbuluso 20:11-15). Ndiyeno adzatsogolera anthu Ake onse ku Mzinda wakumwamba, Yerusalemu Watsopano, ndipo adzakhala nawo kosatha (Chivumbuluso 21:1-4). |
Atakhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, Paulo anali ndi chiyembekezo chomwechi chimene tirinacho. Tikukhala ndi chiyembekezo chomwechi m’maganizo mwathu, kuyembekeza zaka chikwi ndi Ufumu wa Kumwamba. Iwo amene sanabadwe mwatsopano adzaonongedwa pamodzi ndi kugwa kwa dzikoli, koma ife Akristu obadwa mwatsopano tizakhala ndi kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Chiyembekezo chimenechi zoonadi chidzakhalako. Matupi athu adzakhala angwiro ndipo tizakhala ndi kulamulira limodzi ndi Yesu kwa zaka chikwi m’dziko latsopano. Poyang’ana kutsogolo kwa tsiku limenelo, tingakhale ndi chiyembekezo ndi kukhala opanda mantha m’dziko lino.
Tiyeni tikhale opirira ndi kudikilira. Ngakhale kuti moyo wathu ndi wotopa, chiyembekezo chathu chidzakhala choona chifukwa timakhulupilira mwa Mulungu. Iwo alibe chiyembekezo alibe ntchito ngati anthu akufa kale. Chonde khalani ndi chiyembekezo ndi kusunga maloto anu mwa kukhulupilira m’mawu a Mulungu.
Monga m’mene chikhululukiro chathu chinali chenicheni, kusintha m’matupi athu kuzakhala kweniweni ndipo ndi zoonadi kuti zolengedwa zonse zizapeza moyo osatha. Chiyembekezo chathunso ndi chenicheni. Khalani ndi chikhulupiliro mu zimene mumakhulupilira. Iwo amene ali ndi chiyembekezo angakhale okongola ndiponso okondwera. Anthu amakhala osakondwa ngati alibe chiyembekezo. Iwo amene alibe maloto alionse alibe chisangalalo chilichonse. Tingakhale ndi moyo osangalala chifukwa tili ndi chiyembekezo cha zaka chikwi ndi Ufumu wa Kumwamba, kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Olungama ayenera kukhala ndi chiyembekezo ndi kulalikira chiyembekezo chimenechi mwa Mzimu Woyera. Tiyenera kuyembekezera kuti uthenga wabwino wathu ukufalikira pa dziko lonse lapansi. Ngati muli ndi chikhulupiliro cholimba, muzazindikira kuti dziko lapansi silaikulu kwambiri. Ngakhale kuyamba kwathu kunali kopanda pake, tizakwanitsa kulalikira uthenga wabwino pa dziko lonse lapansi ngati tiri ndi chiyembekezo cha chipiriro. Monga m’mene Paulo anachitira, tiyenera kukhulupilira.
Iwo amene ali ndi chiyembekezo ndi okhulupirika m’ntchito zawo za kulalikira uthenga wabwino okoma. Tiyenera kukhala ndi chiyembekezo kuti uthenga wabwino ulalikidwe m’nyego ino yopanda chiyembekezo. Tiyenera kulalikira uthenga wabwino okoma kwa okwezedwa, opanda chiyembekezo, osuka ndiponso odzichepetsa. Tiyenera kuwaombola ku mdima polalikira za chiyembekezo cha Ufumu wa Kumwamba, kumene okhawo amene anakhululukidwa machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi angalowe. Tiyenera kuwauza iwo kuti akhale ndi chiyembekezo chakuti dziko la Mulungu lidzabwera mwadzidzi ngati mbala nthawi yovutayi ikatha.
Atumiki ndi oyera mtima amene ndi obadwa mwatsopano, chonde lalikirani othenga uwu kufikira kumalekezero a dziko lino, kusunga zolimba chiyembekezo chanu cha Kumwamba. Ngakhale dziko lingagwe mwansanga bwanji, iwo amene ali ndi chiyembekezo sadzaonongedwa chifukwa ali ndi chinthu china chosatha kutsogolo kwa moyo wao wa dziko lapansi. Iwo mwachidziwikire azakhala ndi moyo wachiwiri opatsidwa kwa iwo ndi Ambuye.