(Yoswa 4:23)“Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordano pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anacitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka.”
Kodi chochitika cha Mtsinje wa Yordano chikutiphunzitsa chiyani?
Chimatiphunzitsa kuti Yesu Kristu anachotseratu imfa yoyambitsidwa ndi uchimo ndi chiweruzo chosatirapo ku mtundu wa anthu.
Ndifuna kunena za uthenga wabwino okoma wa choonadi umene umatilola ife kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Pambuyo pa imfa ya Mose, Mulungu anasankha Yoswa ngati mtsogoleri wa Israyeli. Mose anali woimira lamulo m’Chipangano Chakale. Kukanakhala kuti Mose anawoloka Mtsinje wa Yordano ndi anthu a Israyeli ndi kufika ku Kanani, sikukanakhala kofunikira kuti Yoswa akhale mtsogoleri wa anthu. Koma, Mulungu anapanga Mose kufika pamalo omwe ali pafupi ndi Kanani ndi kumupewetsa iye kuti asalowe mkati.
Ambuye athu anatipatsa Mose ndi Yoswa
Mose, oimilira lamulo mu Chipangano Chakale, sanatengere anthu a Israyeli mu Kanani. Kukanakhala kuti anachita zimenezo pamene anali kutsogoleredwa ndi lamulo, zikanakhala kusokoneza chikonzero cha Mulungu cha chipulumutso chathu. Palibe amene angamasuke ku machimo ake pamaso pa lamulo la Mulungu chifukwa palibe amene angasunge lamulo. Pakuti uchimo udziwika ndi lamulo (Aroma 3:20).
Chifukwa chimene Mulungu anapatsira munthu lamulo ndi kumpatsa iye nzeru ya uchimo, kupanga lamulo kukhala mphunzitsi wake ndi kumutengera iye kwa Kristu pofuna kuti akhale wolungamitsidwa ndi chikhulupiliro (Agalatiya 3:24). Popeza lamulo linali ngati njira yopezera Yesu, anthu anali kufuna Yesu, ndipo ichi ndi chifukwa chake Yesu anayenera kubwera padziko lino. Chimene Mulungu anauza Yoswa kuchita chinali kulamula anthu a Israyeli kuwoloka Mtsinje wa Yordano ndi kulowa m’dziko la Kanani.
Mulungu anawatsogolera iwo kulowa mu dziko la Kanani ndi mtsogoleri wawo watsopano, Yoswa, pambuyo pa imfa ya Mose. Yoswa analamula akulu akulu a anthu, kunena, “Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene YEHOVA Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu” (Yoswa 1:11).
Mulungu analamula Yoswa kuti alowe mu Kanani ataona kuti ndikosatheka ndi Mose. Mulungu analamula Yoswa, kunena kuti, “Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m’Yordano. Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israyeli. Idzani kuno, mumve mau a YEHOVA Mulungu wanu. Nati Yoswa, Ndi ici mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapitikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.” (Yoswa 3:8-10).
Pambuyo pa imfa ya Mose, Mulungu anasankha Yoswa mtsogoleri wa Israyeli ndi kumulamula kuti alowe m’dziko la Kanani ndi anthu a Israyeli. Dzina lakuti Yoswa likutanthauza “Mpulumutsi,” mau ofanana ndi “Yesu” kapena “Hosiya.” Mtumiki wa Mulungu, Yoswa analamula ansembe kuti anyamule Likasa la Pangano ndi kuwoloka Mtsinje wa Yordano pamene anali kutsogolera anthu. Pamene ansembe amene ananyamula Likasa analowetsa miyendo yawo m’madzi (popeza Yordano amasefukira pa nthawi yokolola), madzi amene anali kuchokera kumtunda anaima ndipo ananyamuka kutali kwambiri kwa Adamu, mzinda omwe uli kuseri kwa Zaretani. Choncho madzi amene anali kupita pansi pa Nyanja ya Arabani, Nyanja ya Mchere, anadulidwa ndipo anthu anawoloka kupita ku mzinda oyandikana ndi Yeriko (Yoswa 3:15-16).
Kudzera mu chochitika chimenechi, Mulungu akutiphunzitsa kuti anachotseratu imfa imene inabwera ndi uchimo ndi chiweruzo chosatirapo ku mtundu wa anthu. M’mawu ena, Yesu Kristu Mpulumutsi wathu anachotsa machimo onse a mtundu wa anthu pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anapachikidwa. Mwa njira imeneyi, anapulumutsa mtundu wa anthu ku machimo awo mwa kuwatengera ku dziko la Kanani, limene likuimira Ufumu wa Kumwamba.
Mtsinje wa Yordano ndi malo omwe mtundu wa anthu unayeretsedwa
Chochitika cha mbiri yakale ya kuwoloka kwa Mtsinje wa Yordano, monga m’mene kunalembedwa mu Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano, ndi zochitika zofunika kwambiri zimene zikanatengera kuchipulumutso chakumapeto ku matemberero ndi ziweruzo zochokera ku machimo a mtundu wa anthu.
Mtsinje wa Yordano unali kuyerekezedwa ngati Mtsinje wa imfa, ndipo kothera kwake kwa mtsinje kunali Nyanja yakufa. Mawu akuti Yordano akutanthauza “mtsinje umene umathira pansi pokha, kuyandikira ku imfa” kapena “kumizidwa, kupondereza, kusindikiza pansi, kugwa.” Ichi chimaonetsa momveka bwino mbiri ya machimo a anthu. Mu mtsinje umenewu, Yesu, kudzera mu ubatizo Wake, analandira kuyenda konse kwa uchimo kumene sikukanathetsedwa ndi munthu aliyense, ndipo pothera pake anafa pa Mtanda ndipo motero anavomera chiweruzo m’malo mwa anthu chifukwa cha machimowa.
Kodi ife, mbeu za Adamu ndi Hava, tikupita kuti? Popeza zolengedwa zonse zimabadwa ndi uchimo, zimachita uchimo, ndipo monga mphoto ya machimo, zikupita molunjika imfa. Pa mbiri yonse ya munthu, zolengedwa zonse zikupita ku chionongeko kuchokera kukubadwa kwawo. Ngakhale kuti amayesetsa molimba kuti athetse khalidwe lawo la uchimo, sangathetse, ndipo ndi chifukwa chake akuyenda molunjika kufupi ndi chiweruzo chomaliza cha machimo awo.
Koma, Mulungu anadula kuyenda kwa uchimo ndi chiweruzo. Mulungu anatsogolera Yoswa kuti atengere anthu a Israyeli mu dziko la Kanani powoloka Mtsinje wa Yordano. Ichi chinali chifuniro cha Mulungu kwa Yoswa. Nkhaniyi ikusonyeza kuti pofuna kuti timasuke ku uchimo, tiyenera kulipira mphoto yauchimo, imene ndi imfa, ndipo kuti kudzera mwa malipiro amenewa, ndife oyeretsedwa ku machimo athu onse ndi kulowa Kumwamba.
Mu Chipangano Chakale, kusefukira kwa mtsinje kunaimitsidwa, ndipo kunasinthidwa kukhala malo ouma pamene ansembe amene ananyamula Likasa la Pangano analowetsa miyendo yawo m’madzi. Ichi chinalola anthu a Israyeli kuwoloka mtsinje. Ichi chinali chikhululukiro cha uchimo chimene chinaperekedwa kwa okhawo amene anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Unali uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene unalipira mphoto ya uchimo wa mtundu wa anthu, ndipo ife talandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Ngwazi Namani
Namani, amene akuoneka mu mutu 5 wa 2 Mafumu, anali kazembe wa khamu la nkhondo la Aramu amene anapulumutsa dziko lake ku adani ake. Analinso wakhate yemwe akanatha kutaya zonse chifukwa cha temberero. Koma nthawi ina anamva nkhani yokoma kuti angapulumutsidwe ku temberero limeneli. Kunanenedwa kuti angachiritsidwe ngati angapite kukaonana ndi mtumiki wa Mulungu amene anali kukhala ku Israyeli. Anali kapolo wamkazi wamng’ono amene anapereka nkhani imeneyi. Iye anati, “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadamciritsa khate lace” (2 Mafumu 5:3).
Anakhulupilira nkhaniyi ndipo anapita ku Israyeli. Pamene anafika kutsogolo kwa nyumba ya Elisa, Elisa anatuma mthenga kwa iye, ndi kunena kuti, “Kasambe m’Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka” (2 Mafumu 5:10). Popeza anali kuyembekezera machiritso odabwitsa, Namani anakalipa ndipo anaganiza zobwerera ku nyumba ya kudziko lake. Koma, chifukwa cha pempho lofunitsitsa la kapolo wake, anamvera Elisa ndi kupita kukamiza thupi lake lonse kasanu ndi kawiri mu Yordano. Kumeneko, thupi lake linabwereranso, linakhala ngati khungu la mwana wakhanda.
Mwa njira imodzimodzi, tadziwa kuti pofuna kuti tikhululukidwe machimo athu onse, tiyenera kusiya maganizo athu ndi kulola zimene zinalembedwa mu Baibulo. Ndiyeno tizapatsidwa madalitso okoma. Iye amene akufuna kupulumutsidwa ayenera kumvera mawu a Mulungu ndi kukhulupilira mwa iwo kwathunthu.
Baibulo limanena kuti machimo onse adziko anatsukidwa ndi uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Sitiyenera kuganiza mwa njira imodzimodzi monga Namani osamvera. Sitingayeretsedwe ku machimo athu popanda uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Choncho, kuti tikhululukidwe machimo athu onse, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Monga Namani anayeretsedwa pomiza thupi lake kasanu ndi kawiri m’madzi, tikhulupilira kuti tingayeretsedwe ku machimo athu pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu, kupachikidwa Kwake ndi kuukanso Kwake. Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu m’mene ulili.
Chodzidzitswachi mu Mtsinje wa Yordano chinasonyeza mbeu zonse za Adamu ndi dalitso limene linadula kuyenda kwa machimo onse ndi kuthetsa chiweruzo. Anthu onse anachotsedwa mu Munda wa Edeni chifukwa Adamu ndi Hava anachimwa atayesedwa ndi Satana. Komabe, chochitika mu Yordano chinali uthenga wabwino okoma chimene chinatengera mtundu onse wa anthu kubwerera ku Munda wa Edeni.
Chochitika mu Mtsinje wa Yordano
Baibulo linalemba nkhani yokoma yakuti Yesu anachotsa uchimo onse mu Yordano. “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” (Mateyu 3:15). Baibulo limanena kuti machimo onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano. M’mawu ena ubatizo wa Yesu unali chochitika chimene chinadula unyolo wa uchimo umene anamanga mtundu onse wa anthu. Umu ndi m’mene Yesu anathetsera uchimo ndipo pamapeto pake anatipatsa chipulumutso ndi mwazi Wake pa Mtanda.
Yordano unali mtsinje wa ubatizo umene unayeretsa machimo athu onse. Tinatha kukwaniritsa lamulo la Mulungu, “Pakuti mphoto yace ya ucimo ndi imfa” (Aroma 6:23), chifukwa Yesu analipira mphoto pobatizidwa mu Mtsinje wa Yordano ndi kufa pa Mtanda. Uwu ndi uthenga wabwino okoma umene Ambuye athu anapatsa mtundu wa anthu.
Machimo onse a mtundu wa anthu anapitilira kuchokera kwa Adamu, koma anaimitsidwa ndi ubatizo wa Yesu mu Mtsinje wa Yordano ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Palibe uchimo umene unasala zikomo ku ubatizo wa Yesu. Ndi nkhani yodalitsika komanso yokoma chotani imeneyi. Ife, pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu, tapulumutsidwa ku kuzungulira kwa machimo, tayeretsedwa ku machimo onse ndi kukhala oyera mu lamulo la chiombolo la Mulungu. Mwa ichi, ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda ndi uthenga bwabwino umene umapulumutsa mtundu onse wa anthu. Tiyeneradi kukhulupilira mwa ichi. “Ndipo cinthu ciri conse cosaturuka m’cikhulupiriro, ndico ucimo” (Aroma 14:23), akutero Ambuye. Chimodzimodzi, timadalitsidwa pokhapo ngati takhulupilira mu uthenga wabwinowu okoma.
Kodi mudakali ndi uchimo mu mtima mwanu ngakhale kuti uchimo onse unaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa ndi Yohane? Yesu anachotsa machimo onse adziko. Muyenera kulola zimene zinalembedwa mu Baibulo. Uthenga wabwino okhawo wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake a pa Mtanda ndi umene angachotse uchimo wanu ndi kukupewetsani ku imfa yanu ndi matemberero ena onse. Kubatiza kukutanthauza kuti, “Kutsukidwa, kumizidwa, kukwiriridwa, kuperekedwa pa, ndiponso kusamutsidwa.”
Mtundu onse wa anthu ungakhululukidwe machimo awo pokhululupira mu uthenga wabwino okoma opatsidwa ndi Yesu. Ndi chifukwa chake Yesu anazitcha Yekha ‘njira ya Kumwamba.’ Tingalowe Kumwamba ndi kukhala ndi moyo osatha pokhulupilira mwa Iye. Iye ndi Ambuye wathu, amene anatipatsa ife kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Tinakhululukidwa ku chiweruzo chonse cha machimo athu pokhulupilira mu ubatizo Wake ndiponso mwazi.
Temberero linatha ndipo mtsinje unakhala malo ouma chifukwa wansembe amene ananyamula Likasa la Pangano analowetsa miyendo yake m’madzi mwa chikhulupiliro. Ichi chinali chimene Mulungu anakonza, ndipo ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda anakwaniritsa chikonzerochi. Kodi ndi uthenga wabwino okoma chotani umenewu. Ili linali lamulo lachipulumutso ndipo popanda limeneli chipulumutso chathu chinali chosatheka. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okomawu tsopano angawoloke Mtsinje wa Yordano ndi kulowa mu dziko la Kanani. Kuti madzi anauma kotheratu kukutanthauza kuti machimo onse a dziko anaperekedwa kwa Yesu ndipo Iye anaweruzidwa kamba ka ife. Uwu ndi uthenga umene umatipatsa kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Mulungu, amene analenga mtundu wa anthu, amadziwa kuti muyezo wa nzeru za munthu uli pakatikati pa 110 kufika pa 130 basi. Choncho, sangasokoneze choonadichi cha kulandira Mzimu Woyera. Mulungu anachotsa machimo awo onse ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake pa Mtanda. Iye anapangitsa kukhala kotheka kuti tilandire Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera kotero kuti onse a iwo audziwe. Muzazindikiranso kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino okomawu.
Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mu Baibulo, sitingalandire Mzimu Woyera pongopemphera mapemphero a kulapa. Anthu amaganiza kuti Mzimu Woyera ndi chinthu chimene chimapatsidwa ngati apemphera mitundu yosiyanasiyana ya mapemphero. Koma ichi sichinthu choona. Mzimu Woyera umapatsidwa kwa okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma, ndipo ukufunika kuwapanga iwo kukhala ana a Mulungu. Uko ndiko kunena kuti, kukhazikika kwa Mzimu Woyera chinali chidziwitso kuti munthu anakhala mwana wa Mulungu. Mulungu amapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma kuonetsetsa kuti ndi ana Ake.
Ngati anthu akhulupilira mwa Yesu koma sakudziwa kapena kukhulupilira mu uthenga wabwinowu okoma, sangakhale olimbitsidwa mu choonadi chakuti machimo awo onse anaperekedwa kwa Iye. Choncho, anthu onse ayenera kudziwa ndi kukhulupilira kuti ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi uthenga wabwino okoma umene unachotsa machimo awo.
Ndani amachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko? Yohane Mbatizi amatero. Kuti anabatizidwa ndi Yohane ndi kuchotsa machimo onse adziko ndi zimene Mulungu Atate wathu anakonza (Levitiko 4:13-21, 16:1-30). Kodi ndani anakwaniritsa chikonzero Chake? Yesu anachita zimenezo. Kodi ndani pomaliza anatsimikiza chikwaniritso cha chikonzerochi? Mzimu Woyera amatero. Mulungu mu Utatu anakwaniritsa chikhululukiro cha uchimo ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake wa pa Mtanda kutipanga ife kukhala ana Ake. Mzimu Woyera umakhala mwa ife ndipo umatsimikiza kuti tinapulumutsidwa ku machimo athu onse pamene Yesu anakwaniritsa chikonzero cha Mulungu.
Kodi zinthu m’dziko lino zimaoneka kukhala zovuta kwambiri? Ndipo maganizo anu ndi osokonekera motani? Munthu sangakhulupilire mu uthenga wabwino okomawu ngati sanasiye maganizo ake. Chiphunzitso cha Chikristu cha masiku ano chimene anthu ambiri amachikhulupilira ndi chakuti ‘tchimo loyambirira linachoka, koma machimo amasiku onse amakhululukidwa ngati munthu wapemphera mapemphero akulapa.’ Koma, ichi chiri kutali ndi choonadi chathunthu; mwa choonadi ndi uthenga wabodza. Ngati mungakhulupilire mwa iwo, simungamvetsetse Baibulo kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto, ndipo pamene nthawi ikupita muzaona zovuta zambirimbiri pamene mukutsatira Yesu. Ndi chifukwa chake mwa Akristu muli ena amene amakhulupilira mu uthenga osiyana ndi Mulungu osiyananso.
Anthu ena amanena kuti amalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwa ‘kupemphera.` Zikuoneka monga ndi zomveka, koma Baibulo limanena kuti Mzimu Woyera unatsikira pa Yesu ngati nkhunda pamene anabatizidwa ndi kuturuka m’madzi. Uwu ndi uthenga wabwino oona ndipo Mzimu Woyera umabwera pa iwo amene amakhulupilira uthenga wabwinowu okoma.
Kuonjezerapo, anthu ena amanena kuti analandira Mzimu Woyera mwa kupemphera mapemphero a kulapa. Kodi Mzimu Woyera umaperekedwa pamene anthu apempha chikhululukiro? Mulungu ndi Wolungama. Mzimu Woyera sumabwera chifukwa chakuti umawamvera chisoni. Ngakhale anthu angalire kapena kupemphera molimba bwanji, Mzimu Woyera sungabwere pa iwo. Umabwera pa iwo amene amakhulupilira kuti Mulungu anakwaniritsa chikonzero Chake cha kupulumutsa iwo. Muyenera kusunga m’maganizo kuti simungalandire Mzimu Woyera ngakhale mungalire bwanji kwa Mulungu kapena kupemphera molimba bwanji. Mzimu Woyera uli payekha ku chifuniro cha munthu.
Ngakhale mbiri ya zisankho za anthu m’dziko lino ingasinthidwe, koma uthenga wabwino okoma ndi lamulo la kukhazikika kwa Mzimu Woyera sizingasinthe; ndiko kunena kuti sangasinthe, Ngati anthu samvetsetsa uthenga wabwino okoma, ndi kovuta kwa iwo kubwerera ku kuchita chikhulupiliro choona. Ndi chifukwa cha chimenechi kuti anthu ambiri sangalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Kodi mungakhale wokhumudwa chotani ngati munakhulupilira mwa Yesu koma munaonongedwa chifukwa chakuti simunadziwe uthenga wabwino okoma? Baibulo limanena kuti kwa anthu ena uthenga wabwino okoma ndi mwala okhala pangondya ndiponso tanthwe la mlandu.
Ngati mwamvetsetsa chinsinsi cha ubatizo wa Yesu ndi Yohane, mungakhululukidwenso ku machimo anu ndi kukhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Iye anapulumutsa ochimwa onse pobatizidwa, kufa pa Mtanda ndi kuukitsidwa. Chiombolo chomwe Yesu anapereka kwa ife chinali njira yachilungamo ya chipulumutso. Iye anakhala Mpulumutsi oona wa ochimwa onse, ndipo anatsimikizira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Pokhapo ngati mukhulupilira mwa icho!
Kunalembedwa mu Chipangano Chakale kuti pamene ansembe analowetsa miyendo yawo mu Yordano, mtsinje unakhala malo ouma. Ndi chozizwitsa chokwanira kuti madzi anaimitsidwa, koma zozizwitsa zambiri zinali kubwera. Chimene chiri chozizwitsa kwambiri ndi chakuti mtsinje unakhala malo ouma. Chochitika chimenechi chinakhala ngati chochitika cha chipulumutso cha Mulungu, chimene chinatsogolera ku chikhululukiro cha uchimo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Malo ouma akuimira njira imene machimo onse adziko adzakhululukidwa zikomo ku ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Machimo onse anachokera kwa Adamu kufikira mtundu onse wa anthu, koma temberero la chiweruzo linatha ndi ubatizo wa Yesu. Tsopano, chimene tiyenera kuchita ndi kukhululukidwa machimo athu pokhala ndi chikhulupiliro ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Kodi mumakhulupilira m’choonadi chokoma kuti Yesu anachotsa machimo anu onse kudzera mu ubatizo Wake mu Mtsinje wa Yordano?
Muyenera kukhulupilira kuti Yesu Kristu anabatizidwa kuti achotse machimo onse adziko lapansi. Mwa kuonjezerapo, muyeneranso kudziwa, kumvetsa ndi kukhulupilira kufunika kwa ubatizo Wake. Kukanakhala kuti ansembe sanalowe mu Yordano, anthu a Israeli sakanatha kupanga kalowedwe kabwino m’dziko la Kanani. Phazi limodzi loyambilira lolowera m’dziko la Kanani linali kuwoloka Mtsinje wa Yordano. Choncho, pokhapo ngati tawoloka mtsinje ndi Likasa la Pangano ndi pamene tingalowe m’dziko la Kanani. Ichi chimatiphunzitsa kuti munthu angakhululukidwe machimo ake pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu.
Baibulo limanena kuti ubatizo wa Yesu inali ntchito ya Mulungu. Ichi chinachitikanso mogwirizana ndi ansembe. Monga madzi a mu Mtsinje wa Yordano anaimitsidwa pamene ansembe analowetsa mapazi awo m’madzi, anthu adziko apulumutsidwa ku machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwinowu okoma.
Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumapatsidwa mwa chikhulupiliro mu uthenga wabwino okomawu. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda zidzakutsogolerani inu kuti mulandire chikhululukiro cha uchimo komanso Mzimu Woyera. Uthenga wabwino okomawu wa madzi ndi Mzimu ndi ofunikira kuti tipeze kukhazikika kwa Mzimu Woyera.