(Mateyu 27:45-54)“Ndipo ora lacisanu ndi cimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai. Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu anapfuula m’mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine? Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamenew anamva, ananena, Uyo aitana Eliya. Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga cinkhupule, nacidzadza ndi vinyo wosasa, naciika pabango, namwetsa Iye. Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa. Ndipo Yesu, pamene anapfuula ndi mau akuru, anapereka mzimu wace. Ndipo onani cinsaru cocinga ca m’Kacisi cinang’ambika pakati, kucokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang’ambika; ndi manda inatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka; ndipo anaturuka m’manda mwao pambuyo pa kuuka kwace, nalowa m’mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri. Ndipo pamene mkuru wa asilikari, ndi iwo anali naye akudikira Yesu, anaona cibvomezi, ndi zinthu zimene zinacitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyo ndi Mwana wa Mulungu.”
Kodi n’chifukwa chiani nsaru yotchinga m’Kachisi wa Mulungu inang’ambika pakati pamene Yesu anapereka mzimu Wake pa Mtanda?
Chifukwa Ufumu wa Mulungu unatsegulidwa kwa iwo amene amakhulupilira mu ubatizo ndi kupachikidwa Kwake
Kuti tizindikire choonadi cha uthenga wabwino okoma, choyamba munthu ayenera kudziwa ndi kumvetsetsa ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe yomwe inali kuchitika kuti anthu akhululukidwe machimo awo pamaso pa Mulungu mu Chipangano Chakale. Muyenera kudziwa ndi kukhulupilira choonadi chotsatirachi.
Mogwirizana ndi nsembe yakale ya chitetezero cha machimo, monga analembera mu Levitiko mutu 16 mu Chipangano Chakale, mkulu Wansembe anali kuika manja ake pa mbuzi yamoyo ndi kupereka pa iyo machimo onse anachita anthu chaka chonse. Kenako m’malo mwa a Israyeli, nsembe inali kuphedwa, ndipo mkulu wansembe ankawaza mwazi wake pa mpando wachifundo. Ichi chinali kutetezera machimo onse a Aisrayeli. Chimodzimodzi, okhawo amene anakhulupilira mu kuika kwa manja, m’mwazi komanso m’mawu a Mulungu ndi amene anali oyenera kulowa m’malo opatulika.
Ansembe nthawi zonse anali kupita ku malo oyamba a chihema, ndi kuchita ntchito. Koma mu malo achiwiri, malo Opatulikitsa, mkulu wansembe anali kulowa yekha kamodzi pachaka, osati opanda mwazi, umene anali kudziperekera yekha ndi a machimo a anthu amene anachita chifukwa cha kusadziwa (Ahebri 9:6-7). Chimodzimodzi, ngakhale mkulu wansembe sanali kulowa mu malo Opatulikitsa opanda mwazi wansembe omwe unkakonzedwa kudzera mu kuika kwa manja mwa chikhulupiliro.
Monga kunanenera mu Chipangano Chatsopano, Yesu Kristu anaperekedwa nsembe m’malo mwathu
Mu Chipangano Chatsopano, tinauzidwa kuti munthu angolwe mu Ufumu wa Mulungu kudzera mu chikhulupiliro chake cha mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Kodi ndi liti pamene nsaru yotchinga mkachisi wa Mulungu inanga’mbika pakati kuchokera pamwamba kufika pansi? Ndi panthawi imene Yesu anapachikidwa atabwera m’dziko lino ndipo anabatizidwa ndi Yohane.
Kodi pali chifukwa chotani choperekera chimenechi? Yesu anabwera padziko lino ngati nsembe, yotchedwa Mwanawankhosa wa Mulungu, anachotsa machimo adziko lapansi pobatizidwa ndi Yohane, ndipo motero anayeretsa mtundu wa anthu ku machimo awo onse pamene anapachikidwa. Kung’ambika kwa nsaru ndi chizindikiro chakuti machimo onse a mtundu wa anthu amene anatilekanitsa ndi Mulungu anafufutidwa kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi wa pa Mtanda.
Yesu Iyeyekha anaphwanya khoma limeneli mwa kulipira mphoto yauchimo, imene ndi imfa. Yesu anabatizidwa ndi kupachikidwa kuti achotse machimo a dziko. Ichi ndi chifukwa chake nsaru ya m’Kachisi wa Mulungu inang’ambika pakati. Monga m’mene ansembe anali kulowa mu chihema ndi chikhulupiliro mu kuika manja, tsopano tingalowe mu Ufumu wa Kumwamba zikomo ku chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.
Pamene Yesu anapachikidwa, Analira ndi mawu ofuula kwambiri, kunena kuti “Eli, Eli, lama sabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46) Pamene anapereka mzimu Wake, anati, “kwatha!” (Yohane 19:30) Yesu anasiyidwa ndi Atate Ake pa Mtanda kwa nthawi yochepa chifukwa ananyamula machimo onse a dziko kuyambira pa ubatizo Wake ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordano.
Anafa chifukwa cha chipulumutso cha mtundu wa anthu onse. Chifukwa cha ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda, onse amene anali ndi chikhulupiliro mwa Iye anapulumutsidwa. Chifukwa tinabadwa ochimwa ndipo ndife oyenera kuweruzidwa, Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo athu onse.
Chipata cha Ufumu wa Kumwamba chinatsekedwa zolimba kufikira Yesu anafufuta ife ku machimo athu onse. Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda, nsaru yotchinga m’Kachisi inang’ambika pakati kuchokera pamwamba kufikira pansi kotero kuti aliyense amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma alowe mu kachisi wa kumwamba wa Mulungu.
Ndine othokoza kwa Ambuye kuti ndili ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tsopano ndingalowe mu Ufumu wa Kumwamba kudzera mu chikhulupiliro changa mu uthenga wabwino okoma omwe Yesu anakwaniritsa kudzera mu ubatizo ndi mwazi Wake. Sindikanapeza chipulumutso kudzera mu mphamvu zanga, kuchita bwino ndi kuyesayetsa kwanga.
Dalitso limene limatitengera ife mu Ufumu wa Kumwamba silimapezeka kudzera mu mapemphero wamba, zopereka komanso kudzipereka tokha. Munthu angapulumutsidwe ku uchimo pongokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Munthu angalowe mu Ufumu wa Kumwamba pongokhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma. Yesu ndiye chipata cha Kumwamba. Palibe chikhulupiliro china chimene ndi choyenerera kwa iwo amene amakhulupilira mwa Yesu. Khoma la Kumwamba silimaperekedwa ngati malipiro a zopereka zodzipereka, zoyesayesa zadziko kapena zochita zina. Chinthu choyenerera choona cha okhulupilira kuti alowe mu Ufumu ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu mu Mtsinje wa Yordano ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda.
Kukhulupilira m’madzi (ubatizo wa Yesu mu Mtsinje wa Yordano) ndi mwazi Wake (Mtanda) zidzakuperekani inu ku ufumu wa Kumwamba. Munthu amene adakali ndi uchimo mu mtima wake, ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu, ayenera kukhulupilira mu chinthu chimodzi: uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32).
Sitikudziwa ndendende nthawi yathu ya kufa kwathu koma Yesu akudziwa zonse. Popeza anadziwa bwino chibadwidwe chathu chauchimo, anatsuka machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda zaka zikwi ziwiri zapitazo.
Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwinowu okoma umene unag’amba nsaru yotchinga m’Kachisi wa Mulungu
Mpulumutsi anabadwa kwa namwali kuti apulumutse mtundu wa anthu ku machimo awo. Kunali kudzera mu ubatizo Wake ali ndi zaka 30 mu Mtsinje wa Yordano, m’mene Yesu anachotsa machimo onse a dziko. Machimo onse a mtundu wa anthu ochokera ku ofoka zawo ndi zolakwa zinakhululukidwa tikuthokoza Yesu. Ubatizo Wake ndi mwazi ndi mafungulo amuyaya ku chipulumutso cha mtundu wa anthu onse. Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pa Mtanda ndipo tsopano onse amene ali ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino angalowe mu Ufumu wa Kumwamba.
Nsaru ya m’Kachisi wa Mulungu inang’ambika pakati pamene Yesu anapereka mzimu Wake pa Mtanda. Kodi nsaru ya m’Kachisi wa Mulungu ingang’ambike bwanji pakati pamene Yesu anafa pa Mtanda? Chifukwa ndi chakuti chipulumutso cha mtundu wa anthu chinakwaniritsidwa ndi Iye mu uthenga wabwino.
Mu Chipangano Chakale, timaphunzira za chihema cha Israyeli. Pamenepo panali guwa la nsembe zopsereza ndi mkhate. Patsogolo pa mkhate umenewu, panali chihema ndipo mkati mwa chihema kuseli kwa nsaru kunali likasa, kumene kunkakhala Mulungu ndi ulemerero Wake. Nsaru inali youmbidwa molimba kotero kuti akavalo anai okokerana ku ngondya zinai sakanatha kung’amba nsaru yake. Ngakhale kuti Mfumu Solomo anasinthanitsa chihema ndi Kachisi, kapangidwe kake sikanasinthidwe, ndipo nsaru inali pamenepobe kutseka njira ya Malo Opatulikitsa. Komabe, inang’ambika pakati kuchokera pamwamba kufikira pansi pamene Yesu anafa kukhetsa mwazi pa Mtanda. Ichi chikuchitira umboni pa choonadi chakuti ndi wotani uthenga wabwino okoma komanso wangwiro umene unamalizika ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake.
Mulungu anadalitsa mtundu onse wa anthu ndi chikhululukiro cha uchimo ndi moyo osatha, kuwakumbatira iwo ndi uthenga wabwino okoma. Yesu, monga nsembe, analipira mphoto ya uchimo pamene anabatizidwa ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda. Baibulo limanena kuti, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa” (Aroma 6:23). Monga mu nthawi ya Chipangano Chakale, munthu anali kulowa mu Kachisi wa Mulungu ndi mwazi wa nsembe ndi kulandira chitetezero cha machimo, choncho tingapite kwa Mulungu ndi nsembe yathu, imene ndi Yesu, ndi kukhululukidwa zolakwa zathu. Ichi ndi choonadi. Ndipo mawu, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa” akutionetsa m’mene uthenga wabwino okoma ulili wangwiro.
Njira ya Kumwamba ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Kung’ambika kwa nsaru pakati kukutanthauza kutseguka kwa Ufumu wa Mulungu. Pamene tadziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino umenewu, kunena kuti, “Oho, Yesu anachotsa machimo anga onse. Oho, Yesu analipira machimo anga onse pa Mtanda!” chipata cha Kumwamba chidzatsekulidwa pamaso pathu. Kumwamba tsopano ndi kotsegukira iwo amene apeza chiombolo kudzera mu chikhulupiliro chawo mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Mwazi wa Yesu unapulumutsa ochimwa ku imfa ndipo ubatizo Wake unali njira yochotsera machimo a mtundu wa anthu onse.
Dziko linagwedezeka ndipo miyala inang’ambika pamene Ambuye anapereka mzimu Wake pa Mtanda. Pamenepo, mwazi Wake unagwa pansi ndipo anayamba kuyenda kupita pansi. Pamene Yesu anafa pa Mtanda, machimo onse a mtundu wa anthu anayeretsedwa, uthenga wabwino okoma unamarizika, ndipo okhulupirira onse anakhala oyenerera kulowa mu ufumu wa Kumwamba. Ichi ndi choonadi chenicheni cha kubadwa mwatsopano.
Pali aphunzitsi ambiri amene anachita kafukufuku kufufuza m’mene angakanire za kukhalapo kwa Yesu Kristu ngati munthu weniweni. Koma sanapilire kulingalira kwawo molimbana ndi maumboni ochuruka a mbiri ya kupezeka Kwake. Mwa ena a iwo, ambiri anazipereka ndi akhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Anazindikira kuti umboni wa Yesu unali waukuru moti sangakane kukhalapo Kwake. Iwo anavomera Yesu ngati Mpulumutsi wawo pamene anadziwa uthenga wabwino okoma umenewu, otchedwa, kubadwa Kwake, ubatizo, imfa, kuukanso, kukwera kumwamba ndi kubweranso Kwake Kwachiwiri.
Sitinachitire umboni ubatizo wa Yesu. Maso athu sanaone chimene chinachitika zaka 2,000 zapitazo. Komabe, kudzera mu zimene zinalembedwa, aliyense angakumane ndi uthenga wabwino okoma umenewu. Yesu anaphwanya khoma la uchimo pakati pa Mulungu ndi munthu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake, ndipo motero nsaru ya mu Ufumu wa Mulungu inang’ambika pakati kuchokera pamwamba kufikira pansi.
Tsopano aliyense amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene unamarizika ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi, angalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Kodi muli ndi chikhulupiliro mu choonadi chakuti ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi Wake, otchedwa uthenga wabwino okoma umenewu, ndi mafungulo a Ufumu wa Kumwamba?
Ndinali ochimwa nthawi ina, yemwe ndinadalira Yesu kukhala Mpulumutsi wanga koma sindinali kudziwa uthenga wabwino okoma. Komabe, tsiku lina ndinawerenga za chikondi Chake chopanda malire kwa ine mu Baibulo. Ndinadziwa kuti anabatizidwa chifukwa cha ine, kufa pa Mtanda chifukwa cha ine ndipo anaukitsidwa chifukwa cha ine. Yesu anatipulumutsa ife mwa kubatizidwa mu Mtsinje wa Yordano ndipo anapachikidwa kuti alipire mphoto yauchimo chifukwa cha chikondi Chake kwa ife. Takwanitsa kulowa mu Ufumu wa Kumwamba pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu.
Ichi ndi chilungamo chachikulu cha Mulungu ku mtundu wa anthu ndiponso chochitika chofunika kwambiri m’mbiri ya dziko. Utumuki Wake onse – kubadwa Kwake, ubatizo mu Mtsinje wa Yordano, imfa pa Mtanda ndi kuukanso – kunali kupulumutsa ife ku machimo athu onse. Tinayenera ku gehena pambuyo pa kufa kwathu, koma Yesu anapulumutsa miyoyo yathu kuchoka ku gehena wa muyaya ndi kutipatsa uthenga wabwino okoma ngati njira kuti tilowe mu Ufumu wa Kumwamba.
Okondedwa abale, pamene Yesu anafa pa mtanda, msilikali anam’baya ndi mkondo kumbali Kwake, ndipo pomwepo mwazi unaturuka. Izi ndi zomwe zinalembedwa mu Baibulo. Ichi chikuchitira umboni ku choonadi cha uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.
Kodi mukuzindikira kuti chikhulupiliro chanu mu mwazi wa Yesu pa Mtanda ndi chosakwanira kwa inu kukumasulani ku machimo anu onse? Kodi ubatizo wa Yesu ndi ofunika mochepa kapena ndi mwangozi chabe ku chipulumutso chanu? Ngati mumakhulupilira motero, chonde lapani. Tsopano tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi ndi kuona uwo ngati choonadi cha Mulungu.
Kodi mukufuna kuyeretsedwa ku machimo anu onse?
Monga m’mene timafunikira kulipira kuti tituruke mu ngongole, tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi kuti tiyeretsedwe ku machimo athu onse. Sitiyenera kuchita uchimo wakusakhulupirira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ngakhale kuti sitinapereke molunjika machimo athu kwa Yesu, mkhala pakati wotchedwa Yohane Mbatizi anagwira ntchito pa ife.
Pamene Yesu anafa pa Mtanda, manda ena a oyera mtima ku Yerusalemu anatseguka ndipo masiku atatu atatha anaukitsidwa ndi kupita ku Galileya. Chochitika chabwino chimenechi chinachitikadi, koma kunali anthu ambiri amene sanakhulupilire.
Ambuye wathu anapereka Ufumu wa Kumwamba kwa ife, olungama, amene tinalandira chikhululukiro cha uchimo. Tinapulumutsidwa ndi kubadwa mwatsopano, osati kudzera mu mphamvu zathu zathupi kapena kuyesayesa kwa chipembezo, koma kudzera mu chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino okoma. Uthenga wabwino umenewu sinkhani yopeka. Machimo onse a dziko anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa. Munalibe uchimo mwa Iye, koma anayenera kufa pa Mtanda kuti atetezere machimo amene ananyamula pa ubatizo Wake.
Pamene Yesu anapereka Mzimu Wake, dziko linachita chivomezi ndipo tanthwe linang’ambika. Pamene kenturiyo ndi ena anali naye amene anali kulonda thupi la Yesu anamvera chivomezi ndi zinthu zimene zinachitika, anagwidwa ndi mantha akulu, ndi kuchitira umboni kuti, “Indedi Uyo ndi Mwana wa Mulungu” (Mateyu 27:54).
Yosefe munthu wachuma wa ku Arimateya ananyamula thupi la Yesu, kulikulunga mu nsaru yoyera yabwino ndi kuligoneka m’manda ake. Mkulu wansembe ndi Afarisi anapereka ulamuliro kuti manda atetezedwe kufikira tsiku lachitatu.
Komabe, Yesu anaukitsidwa kuti apereke moyo watsopano kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Anapita ku Galileya, kumene analonjeza kuti akakumane ndi ophunzira Ake asanapachikidwe. Zinthu zonsezi – Kubadwa Kwake, ubatizo, kupachikidwa, kuukanso, kukwera ndi Kubweranso Kwake kachiwiri – zinali pa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Inenso ndakhala ochitira umboni amene ndikuchitira umboni kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu wamoyo ndiponso Mpulumutsi wanga.
Kodi uthenga wabwino oona umalalikiridwa kudzera mwa ndani?
Okhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi amachitira umboni ku uthenga wabwino okoma wa choonadi. Uthenga wabwino okoma ukufalitsidwa kudzera mu umboni wa anthu amenewa anapulumutsidwa ku machimo awo. Pamene munthu wamasuka ku machimo ake pokhulupilira mu uthenga wabwino, Mzimu wa Mulungu umayamba kumulamulira iye, ndipo umamusintha mosasamala kanthu za chifuniro chake. Moyo opeza mawu a Mulungu umapitiriza kusintha munthu olungama ndikumupatsa iye ngakhale chikhulupiliro cholimba. Mobwezera, iye amazatamanda Ambuye. Mawu a Mulungu amakhala mwa iye, ndipo chifukwa cha ichi amamvera kusintha kwa mkati mwake tsiku ndi tsiku. Pamene akumuona iye kusintha motero, anthu amachitira umboni kuti, “Iye ndi munthu oomboledwadi. Anakhala m’Kristu weniweni ndiponso mwana wa Mulungu.”
Ngakhale mdierekezi amavomereza ndi kugonja ku uthenga wabwino okoma. “Ndachititsidwa manyazi!” amatero. Koma ndi zoonadi kuti mulibe uchimo m’dziko. Palibe ali ndi uchimo mu mtima mwake.” Motero, mdierekezi amagwira ntchito m’maganizo a anthu, kusokoneza miyoyo yawo yachikhulupiliro. Ntchito ya mdierekezi ndi kupewetsa iwo kuti asalandire madalitso a uzimu a uthenga wabwino.
Satana anagonjetsedwa kwathunthu pa nkhondo ndi Yesu. Satana anapambana pamene Yesu anapachikidwa mwa kulamulira nzeru za anthu. Koma, Yesu anali atachotsa kale machimo a dziko pamene anabatizidwa, ndipo pamene anafa pa Mtanda kuti alipire mphoto ya uchimo. Pa chifukwa ichi, Iye anapulumutsa kwathunthu onse okhulupilira mu uthenga wabwino.
Mdierekezi sanathe kutsekereza chikonzero cha Mulungu chopulumutsa mtundu wa anthu ku machimo awo. Yesu analipira machimo a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi kuti amalizitse uthenga wabwino okoma. Tsopano mulibe uchimo m’dziko lino. Yesu anachotsa uchimo onse kudzera mu ubatizo Wake ndi kuthetsa uchimo onse kudzera mu imfa Yake pa Mtanda, kunena kuti, “Kwatha!” (Yohane 19:30) Satana anachotsedwa mphamvu za kuneneza iwo amene ali ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma. Yesu anagonjetsa mdierekezi kudzera mu kubadwa Kwake, ubatizo, kupachikidwa ndi kuukanso.
Kodi mudakali ndi uchimo mu mitima yanu? Ai. Akristu anganene molimba kuti, “Ndiribe uchimo mu mtima mwanga” kuchokera pa chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino okoma wa choonadi. Munthu amene amakhulupilira mu uthenga wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi alibe ngakhale katchimo kakang’ono mu mtima Wake.
Tsopano uthenga wabwino okoma wakhazikitsidwa mu mitima yathu. Tsopano tikuima omasuka ku zokhumudwitsa zonse pa maso pa Mulungu. Kodi inu nonse mumakhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo anu onse kudzera mu ubatizo Wake mu Mtsinje wa Yordano? Ngati ndi choncho, chiyamiko chanu kwa Mulungu ndiponso chimwemwe chidzakhala chodzala. Mwa kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma, tayeretsedwa ndi kumasuka ku machimo mu dziko lino. Tikuthokoza Mulungu.
“Amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa cikondi cace; amene tiri nao maomboledwe mwa Iye, m’kukhululukidwa kwa zocimwa zathu” (Akolose 1:13-14). Aleluya, tamandani Ambuye.
Yesu anatsegula chipata cha chipulumutso kudzera mu uthenga wabwino okoma. Inunso muyenera kuphwanya khoma mu mtima wanu kamodzi kokha ndi mphamvu ya uthenga wabwino okoma, monga nsaru yotchinga ya m’Kachisi inang’ambika pakati. Uthenga wabwino okoma unapangidwira inu ndi ine. Tingalowe mu Ufumu wa Kumwamba pokhulupilira mu uthenga wabwino umenewu, ndipo ndi choonadi chomaliza chimene chimatilola ife kuti tipeze kukhazikika kwa Mzimu Woyera.