(Yohane 20:21-23)“Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu. Ndipo pamene anati ici anapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera. Zocimwa za anthu ali onse mudzawakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.”
Kodi Ambuye anapereka ulamuliro otani kwa Olungama?
Iye anawapatsa ulamuliro wa kukhululukira machimo ali onse kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Yohane mutu 20 muli zolembedwa za kuukanso kwa Yesu. Ambuye wathu anaukanso kwa akufa ndipo anauza ophunzira Ake kuti, “Landirani Mzimu Woyera.” Ophunzira a Yesu analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngati Mphatso yochokera kwa Iye. Yesu anapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi moyo osatha kwa iwo amene anakhulupilira kuti ubatizo Wake ndi mwazi zinatsuka machimo awo. Baibulo limanena kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha chipulumutso, kutanthauza kuti ubatizo Wake unapulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo awo (1 Petro 3:21).
Kodi n’chifukwa chiani Yesu anabatizidwa?
Kodi n’chifukwa chiani Yesu anabatizidwa ndi Yohane? Yankho la funso limeneli lingaoneka bwino pa zimene Yesu ananena mu Mateyu 3:15, “Pakuti kuyenera kwa ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” apa, “motero” akutanthauza kuti Yesu anachotsa machimo a dziko lapansi pamene Iye anabatizidwa. Ubatizo Wake unachitika mwa njira yofanana monga m’mene kuika manja kunkachitikira mu nthawi ya Chipangano Chakale. Cholinga cha ubatizo Wake chinali kupereka machimo a dziko kwa Yesu.
Kodi tanthauzo la “Chilungamo chonse” ndi chiani? Kodi mawu akuti “kuyenera” akusonyeza chiani? “Chilungamo chonse” akutanthauza kuti kunali koyenera kwa Yesu kuchotsa machimo adziko kudzera mu ubatizo. Ndipo “kuyenera” kukusonyeza kuti yonseyi inali njira yoyenera m’maso mwa Mulungu.
Yesu anachotsa machimo onse a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake ndi kufufuta iwo kwa amene anakhulupilira mwa Iye. Yesu anabatizidwa ndipo anapachikidwa mu chiweruzo cha machimo awo. Uwu ndi uthenga wabwino wa chikhululukiro cha uchimo. Chilungamo cha Mulungu ndi chikhululukiro cha uchimo chimene chinafafaniza machimo onse a ochimwa.
Ngati anthu akufuna chinsinsi cha ubatizo wa Yesu monga kunalembedwa mu Mateyu 3:13-17, adzatha kulandira chikhululukiro cha machimo ndiponso Mzimu Woyera. Zimene Yesu anachita mu utumiki Wake wapagulu ubatizo Wake, kupachikidwa ndi kuukanso kunali kutipatsa njira ya chilungamo yopita ku chipulumutso, monga kunakonzedweratu ndi Mulungu. Mwa njira imeneyi, Yesu anakhala Mpulumutsi oona wa ochimwa onse. Uthenga wabwino wa ubatizo Wake ndiponso mwazi ndi wa chipulumutso, umene unatsuka machimo athu onse.
Anthu angalandire Mzimu Woyera pokhapo ngati adziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi. Chifukwa ubatizo wa Yesu unachotsa machimo onse a dziko, machimo athu anaperekedwa pa Iye. Imfa Yake ya pa Mtanda m’malo mwa mtundu wa anthu inali imfa yanga, ndipo kuukanso Kwake kunali kuukanso kwanga. Mwa ichi, ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda ndi uthenga wabwino wa chikhululukiro cha uchimo ndiponso wa kulandira Mzimu Woyera.
Ndikhulupilira kuti mwaphunzira chifukwa cha ubatizo wa Yesu ndipo muli ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino. Ndiyeno, machimo anu adzafufutidwa ndipo muzalandira Mzimu Woyera. Kodi ndi chifukwa chiani Yesu anabatizidwa? Chinali kufuna kuchotsa machimo onse a dziko. “Pakuti kuyenera kwa ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” (Mateyu 3:15). Ameni, Alleluya!
Lero, ena amakhulupilira kuti kulankhula m’malilime ndi chidziwitso cha kulandira Mzimu Woyera. Koma, chidziwitso choona cha chimenechi ndi chikhulupiliro cha mtengo wapatali mu uthenga wabwino okoma chokhala m’mitima mwa iwo amene analandira moona Mzimu Woyera.
Ambuye anapatsa ulamuliro wokhululukira uchimo kwa anthu onse olungama
Ambuye anapatsa ophunzira Ake ulamuliro wokhululukira uchimo, kunena kuti, “Zocimwa za anthu ali onse mudzawakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa” (Yohane 20:23). Ichi chikusonyeza kuti pamene ophunzira ankalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, machimo a onse amene akumvetsera ndi kukhulupilira anali kukhululukidwa. Komabe, ichi sichikutanthauza kuti akanatha kukhululukira machimo a aliyense, mosasamala kanthu za chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Ophunzira a Yesu anali ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo a ali onse kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Motero, ngati iwo akuphunzitsa zimene zinalembedwa, tiyenera kukhulupilira. Muyenera kukhulupilira kuti Yesu Kristu anapereka uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa inu kuti afafanize machimo anu onse. Pokhapo ndi pamene mungapeze chikhululukiro cha uchimo ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Yesu anatipatsanso ife mphamvu za kupulumutsa anthu onse ku machimo awo polalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Mphamvu za wolamulira a dziko
Kale kale, kumene ndinali kukhala, tinali kuyenda ndi galimoto pa msewu wafumbi. Anthu anali kuturuka m’galimoto pamalo ena ndi kuikankha kukweza phiri. Tsiku lina Mtsogoleri wa dziko wa Korea anabwera ku mwambo otsegulira mphamvu ya magetsi pa msewu umenewo. Anthu anamulandira mtsogoleri posesa msewu ndi kuika mitengo mbali mwake pamene anamva nkhani. Pamene tsiku linafika, thuthumula zinali kutsogolera njira ndipo pambuyo pake pankabwera galimoto la mtsogoleri. Chikhamu cha anthu chinabwera kuzamulonjera ndi mbendela za dziko m’manja mwawo. Kunanenedwa kuti mtsogoleri wa dziko ananena kuti, “Njira iyi ndi yopapatiza, iyenera kukonzedwa.” Masiku ochepa atapita, msewu unakonzedwa ndi phula.
Kodi ndi chiani chinachitika apa? Mawu amodzi ochokera kwa mtsogoleri wa dziko anali okwanira kupangitsa kusintha kwa kaonekedwe ka msewu umenewu. Ulamuliro wa mtsogoleri unali ndi mphamvu kwambiri. Koma, tikudziwa bwino kuti uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe unapatsidwa kwa ife ndi Kristu ndi wa mphamvu kwambiri. Tiyenera kukhulupilira kuti uthenga wabwino umenewu uli ndi mphamvu ya kumasula ife ku machimo onse pa moyo wathu onse.
Ulamuliro oona wa Kukhululukira machimo
“Zocimwa za anthu ali onse mudzawakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.” Ophunzira a Yesu analakira uthenga wabwino kuti machimo awo onse anakhululukidwa. Iwo anauza anthu, “Yesu anafafaniza machimo onse a dziko mwa ubatizo Wake ndi mwazi. Palibe chimene tingadere nkhawa. Ngakhale kuti ndinu oyenera kuchimwa mtsogolo, Yesu anachotsa kale machimo anu a masiku onse ndi kukhetsa mwazi chifukwa cha inu pa Mtanda atabatizidwa ndi Yohane. Yesu anapulumutsa inu! Muyenera kukhulupilira chimenechi!”
Ochimwa anapatsidwa chiombolo pomvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kudzera mwa ophunzira a Yesu. Yesu anapatsa ophunzira Ake ulamuliro wa kukhululukira uchimo kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Chifukwa ophunzira a Yesu analalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kwa anthu onse a m’dziko lapansi, okhulupilira analandira chikhululukiro cha uchimo. Yesu anawapatsa mphatso imeneyi pamodzi ndi ulamuliro wa kukhululukira uchimo.
Anthu ambiri anawerenga mabuku amene ndinawasindikiza posachedwapa, ndipo anapulumutsidwa ku machimo awo atawerenga. Ena anavomereza kuzindikira kwawo kuti chifukwa chimene Yesu anafa pa Mtanda chinali chotsatira cha ubatizo Wake kuti achotse machimo onse a dziko, potenga mawu, “Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natunduzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu” (Yesaya 53:5).
Iye ataukitsidwa, Yesu anati kwa ophunzira Ake, “Landirani Mzimu Woyera. Zocimwa za anthu ali onse mudzawakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa” (Yohane 20:22-23). Yesu anawapatsa ulamuliro wa kukhululukira anthu machimo.
Tinali omangidwa ndi chisokonezo, kupanda kanthu komanso uchimo tisanakhulupilire mu choonadi chimenechi. Koma, tsopano popeza tiri ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi, ndipo ndife omasuka ku uchimo, ndife amene tiyenera kulalikira uthenga wabwino umenewu kwa ena. Kuonjezerapo, Ambuye wathu anapatsa ophunzira Ake mtendere. Ambuye wathu anapatsanso ife mtendere ndi madalitso a Mzimu Woyera. Kuti tilandire mtendere ndi Mzimu Woyera kwa Mulungu, tiyenera kulandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wa pa Mtanda.
Chimene chitimasula ife ku uchimo ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ichi ndi chikhulupiliro cha uzimu chimene chimabweretsa madalitso a kumwamba. Koma chikhulupiliro chosaganizira ena chochokera ku maganizo a munthu chimatsogolera iye ku chionongeko. Tiyenera kupeza chiombolo pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo motero kulandira Mzimu Woyera. Kuti tikhale ndi chikhulupiliro chotere, tiyenera kusiya maganizo athu a dziko lapansi ndi kutembenuza chikhulupiriro chathu ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kuti tikhale ndi chikhulupiliro chofunikira kuti tilandire Mzimu Woyera, munthu ayenera kuvomera uthenga wabwino kuti Yesu anabatizidwa ndi kupachikidwa m’malo mwathu. Ambuye anatipatsa chikhululukiro cha uchimo, mtendere ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa timakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iye anapatsa ophunzira Ake kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi ulamuliro wokhululukira machimo a ali onse amene wakhululupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Tinalandiranso Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino umenewu. Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu wathandiza ena ambiri kuti achite chimodzimodzi. Pamene tikulalikira uthenga wabwino kwa woyandakana nawo kumanso kudziko, iwo amene akuutengera mu mtima amapatsidwa Mzimu Woyera. Ngati uthenga wabwino umene timalalikira supangitsa anthu kulandira Mzimu Woyera, ndiye kuti siuthenga oona. Kumbali inayi, ngati uthenga wabwino omwe timalalikira ungatsogolere iwo kulandira Mzimu Woyera, uthenga wabwino umenewo ndi weniweni.
Ndife odalitsika ndiponso oyamikira motani kukhala ndi uthenga wabwino otere. Uthenga wabwino umene wakhala ukulalikidwa ndi inu komanso ine ndi wangwiro ndiponso wokwezeka. Koma mwatsoka, ndi kovuta kupeza munthu amene amadziwa moona ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino umenewu lero. Motero, tiyenera kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Tiyenera kuthandiza anthu kulandira Mzimu Woyera.
Iwo amene ananyengedwa ndi Satana kuti akane uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu
Tikuthandiza ngakhale iwo amene anakhulupilira kale mwa Yesu. Ambiri a iwo sanalandirebe Mzimu Woyera ngakhale kuti akukhulupilira mwa Yesu. Choncho timathandiza iwo polalikira uthenga wabwino ndipo motero timawathandiza iwo kuti alandire Mzimu Woyera.
Ngati munthu sanalandire Mzimu Woyera ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu, muyenera kukhala mavuto ena mu chikhulupiliro chake. Okhawo amene ali ndi Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro chawo mwa Yesu angaonedwe ngati anthu amene ali ndi chikhulupiliro choona. Motero, tonse tiyenera kusunga chikhulupiliro chimene chimatitsolera ife kuti tilandire Mzimu Woyera. Tiyenera kudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, chifukwa chakuti choonadi chokha cha uthenga wabwino umenewu ndi chimene chimatipangitsa kulandira Mzimu Woyera.
Timalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kotero kuti ena angalandire Mzimu Woyera. Koma, iwo amene amalalikira uthenga wabwino ali oyenera kukumana ndi mavuto ambiri. Akristu ena amaganiza kuti angalandire Mzimu Woyera poyesetsa kwa nthawi yoikika. Ali ndi zoyesa zosokoneza zambiri zomwe sizifunika kwa iwo kuti alandire Mzimu Woyera. Motero nthawi yambiri komanso kudzipereka kukufunika kwambiri kuti tiunikire iwo ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kodi ndani amene sadzakhulupilira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ngati aliyense akuganiza kuti munthu angalandire Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro cha uthenga wabwino umenewu? Satana ananyenga anthu ndi uthenga wabwino usanabwere uthenga wabwino oona. Anthu otere amadabwa kuti pali chiani chosiyana khulupilira pamene iwo amadziona kale kuti iwo okha amakhulupilira mu uthenga wabwino wa Yesu. Motero, amakana ndipo samafuna uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Anthu ambiri m’masiku ano ndiponso chaka samavomera kwanthunthu uthenga wabwino oona wa madzi ndi Mzimu, popeza Satana wawaphimba kale iwo m’maso. Zotsatira zake, amaganiza kuti kukhulupilira mwa Yesu ndi ntchito yosavuta. Koma, kuti timvetsetse bwino choonadi cha uthenga wabwino sichinthu chosavuta konse. Uthenga wabwino oona wa madzi ndi Mzimu unatchingidwa ndi uthenga wabodza.
Anthu amaganiza kuti aliyense angalowe mu Ufumu wa Kumwamba ngati angamapezeke pa mpingo ndi kuulula kuti amakhulupilira mwa Yesu. Ambiri amakhulupilira kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumapatsidwa kudzera mu mphamvu zawo, monga kupemphera ndi kusala kudya. Koma, chikhulupiliro chotere chili kutali ndi choonadi cha kulandira Mzimu Woyera. Iwo amaganiza kuti kunenera m’malilime ndi zozizwitsa zina ndi zizindikiro za kulandira Mzimu Woyera.
Motero, amazindikira kuti tilandire Mzimu Woyera, ndi kofunika kukhulupilira mu uthenga wabwino oona wa madzi ndi Mzimu. Koma, Baibulo limanena kuti munthu angalandire Mzimu Woyera pokhapo mwa kukhulupilira mu mawu a Mulungu. Mulungu anabisa chinsinsi cha kulandira Mzimu Woyera mu mawu Ake.
Iwo amene akufuna kukhazikika kwa Mzimu Woyera
Nthawi ina ndinapita ku Taiwani ndi ogwira nafe ntchito ena. Anthu kumeneko anatipempha mabuku a Mzimu Woyera. Chinthu chimodzimodzi chinachitikanso ku Japani ndi ku Rusia. Chifukwa chimene anthu ambiri amafunira mabuku a kukhazika kwa Mzimu Woyera ndi chakuti anthu a lero amafunitsitsa kwambiri kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Anthu ambiri amakhulupilira mwa Yesu ndipo nthawi zina samadziwa kuti mwina alandira moona Mzimu Woyera, chifukwa alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Kuli anthu ambiri amene amakhulupilira mwa Yesu ndi kunena kuti analandira Mzimu Woyera. Koma, anthu amene analandira Mzimu Woyera mwachikhalire ndiponso kwamuyaya ndi osowa. Anthu ambiri akulephera kuchita choncho posatengera chikhulupiliro chawo mwa Yesu, ndipo ndi chifukwa chake akufunitsitsa kuchita choncho tsopano.
Mwa Akristu a dziko lino, muli anthu ambiri amene amaganiza kuti ali ndi Mzimu Woyera. Ena amanena kuti anakumana ndi Yesu m’maloto mwawo, ndipo ena amanena kuti ali ndi Mzimu Woyera mwa iwo chifukwa achita zinthu za kuthamangitsa ziwanda. Choncho, pali anthu ambiri amene chikhulupiliro chawo chagona pa zokumana nazo zawo. Koma, sikawirikawiri anthu otere amene amalindira moona kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Nthawi ina ndinaganiza kuti ndizoopsa kuti munalibe mabuku m’dziko lino opezera kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro mu uthenga wabwino oyera wa madzi ndi Mzimu. Anthu ambiri amanena za kudziwa kwawo Mzimu Woyera, koma kodi ndi chifukwa chiani palibe mabuku a kukhazikika kwa Mzimu Woyera? Mabuku otere ndi ovuta kupeza, ngakhale kuti mutaona kutali ndiponso mozungulira dziko lonse lapansi.
Iwo amene anakakamira molakwitsa kuti analandira Mzimu Woyera amanena kuti anakumana ngakhale ndi Yesu maso ndi maso ndipo anapita mu Ufumu wa Kumwamba ndi gehena. Iwo anakakamira kuti Yesu ananena kuti, “Mwabwera nthawi isanafike. Muli ndi zambiri zofunika kumaliza m’dziko lanu, choncho fulumirani kupita kumene mumakhala.” Zinthu zotere ndi zosatheka. Koma, kodi Yesu amene anakumana naye angakhale Yesu oona? Kodi Yesu angakumane nawo pamene adakali ndi uchimo m’mitima yawo? Kodi Yesu amakhala mwa munthu ochimwa?
Ndi zoona Akristu ambiri lero alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngakhale kuti akusungabe chikhulupiliro mwa Yesu. Choncho ife, amene tiri ndi Mzimu Woyera mwa ife, tiyenera kufalitsa uthenga wabwino umene udzatsogolera ena kuti alandire mphatso imeneyi. Aliyense akufunika kulandira Mzimu Woyera, ndipo kuti achite zimenezo, chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi chofunika. Pakuti pongokhulupilira mu uthenga wabwino ndi pamene munthu angalandire Mzimu Woyera. Kudzera mu uthenga wabwino wa choonadi umene tonse tikuuzidwa, tingalandire kwa Mulungu mphatso ya Mzimu Woyera.
Tiyenera tonse kuthokoza ndi kutamanda Ambuye pakutipatsa ife uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ndinali ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera pamene Iye anapambana pa ine kuti ndilembe buku limeneli. Pamene buku limeneli lidzasindikizidwa, anthu ambiri adzalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiriro chawo mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira?” (Macitidwe a Atumwi 19:2) Anatero Paulo kwa amene adzakhala ophunzira mu Efeso.
Ife tonse tiyenera kulandira Mzimu Woyera. Akristu kuzungulira dziko lonse lapansi makamaka akufunika kulandira Mzimu Woyera pa nthawi ino yovuta m’mbiri ya dziko. Ndikulalikira njira ya m’baibulo yolandilira Mzimu Woyera, monga Mzimu Woyera ukutsogolera ine kuti ndichite. Kuti mukhale ndi moyo okhutitsidwa, muyenera kukhulupilira mu choonadi cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Popeza ndi mwayi wanu omariza kuti mulandire Mzimu Woyera pansi pa mtima wanu.
Ndikumva kukakamizidwa kufalitsa uthenga wabwino umene umathandiza aliyense kulandira Mzimu Woyera chifukwa Yesu Kristu anandipatsa ine uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kundipatsa ine mphatso ya Mzimu Woyera.
Anthu amitundu ina ayeneranso kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu
Baibulo limafotokoza m’mene ophunzira a Yesu analolera ena kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ngakhale anthu amitundu ina anayenera kusunga chikhulupiliro chomwechi monga ophunzira kuti alandire Mzimu Woyera. Kuonjezerapo, anthu amitundu ina makamaka anayenera kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, chimene ophunzira anali nacho, kuti alowe mu dziko la Mulungu. Motero ife, amene ndife anthu amitundu ina, tiyeneranso kukhulupilira mu uthenga wabwino oona kuti tilandire Mzimu Woyera. Mulungu anatuma Petro kwa Korneliyo, amene anali munthu wa mtundu wina, pofuna kuti azaunikiridwe ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene ndi ofunika kuti alandire Mzimu Woyera.
Ayuda okhulupirika anadabwa kumvera kuti mphatso ya Mzimu Woyera inaperekedwa pa anthu amitundu ina. Pamene Petro anabwerera ku mpingo wa ku Yerusalemu atatha kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, iwo amene anali odulidwa anamudzudzula iye. “Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.” (Macitidwe a Atumwi 11:3) koma Petro anafotokoza zonse kwa iwo kuyambira pachiyambi.
Kufotokoza kwake kunalembedwa mu Macitidwe a Atumwi 11:5-17. “Ndinali ine m’mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m’kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera ciri kutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pa ine; cimaneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga. Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye. Koma ndinati Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m’kamwa mwanga ndi kale lonse. Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m’mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba. Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zanakwezekanso zonse kumwamba. Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m’mene munali ife, anatumidwa kwa ine ocokera ku Kaisareya. Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m’nyumba ya munthuyo; ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m’nyumba yace, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro; amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse. Ndipo m’mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja. Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera. Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?”
Petro ananena kuti sanapite kokha kwa anthu osadulidwa ndi kudya nawo, iye anawauzanso uthenga wabwino zikomo potsogozedwa ndi Mzimu Woyera. Pamene iwo anamva zinthu zimenezi anakhala chete, ndipo analemekeza Mulungu, amene anapereka kulapa ndi moyo kwa iwo onse Korneliyo, abale ake ndi anzake apafupi.
Uthenga wabwino wa utumwi wolandilira Mzimu Woyera
Kodi ntchito yayikulu ya atumwi ndi yotani?
Kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti iwo alandire Mzimu Woyera.
Kodi Atumwi analalikiradi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu? Tiyenera choyamba kutsimikiza ngati mtumwi Petro anakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mu Baibulo, Petro anati, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico - ubatizo” (1 Petulo 3:21). Mtumwi Petro anakhulupilira kuti Yesu anapulumutsa ochimwa onse ku machimo awo pamene anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda. Iye anakhulupiliranso kuti pamene Yesu anabatizidwa (Mateyu 3:15), machimo onse anaperekedwa pa Iye, popeza anapachikidwa ndipo patsogolo pake anaukitsidwa kuti apulumutse ife tonse.
Masiku ano kuli anthu amene ali ndi chikhulupiliro monga cha Petro. Iwo amene amalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi amene amalalikira uthenga wabwino wofanana monga m’mene Petro anachitira. Choonadi chimenechi ndi chokwanira kulola omvetsera onse kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Monga anthu ambiri analandira Mzimu Woyera pamene Petro analalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, tikuonanso anthu akukhulupilira mu uthenga wabwino ndi kulandira Mzimu Woyera pamene tikulalikira choonadi chomwechi. Munthu samalandira Mzimu Woyera pokhulupilira mosadziwa kuti munthu adzapita kumwamba ngati amakhulupilira kokha mwa Yesu ngati Ambuye wake, koma m’malo mwake pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Petro nthawi ina anaona anthu a mitundu ina ngati nsikidzi zomwe zimayenda pansi. Mogwirizana ndi lamulo, anali ngati nyama zodetsedwa Yesu asanabatizidwe, kufa pa Mtanda ndi kuukitsidwa. Komabe, ngakhale Anthu a mitundu ina akanadalitsidwa ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Choncho mawu analankhula kwa Petro, kunena kuti, “Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba” (Macitidwe a Atumwi 10:15).
Ife, monga Anthu a mitundu ina, sitinathe kulandira Mzimu Woyera koma tingakhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwa kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pamene tikulalikira uthenga wabwino mopirira kwa anthu odzala ndi maganizo awo, nthawi zambiri timaona iwo akukhulupilira mu uthenga wabwino ndipo pomaliza amalandira Mzimu Woyera pothera pake. Tingaonenso iwo kuvomereza kuti alibe uchimo m’mitima yawo atakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Ndi pokhapo pamene Mzimu Woyera umakhala mwa Iwo.
Cholinga chathu polalikira uthenga wabwino umenewu si kupangitsa ena kumvetsetsa wamba, koma kuwatsogolera iwo kuti alandire Mzimu Woyera. Choona chakuti iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino umene timalalikira akhululukidwa machimo awo onse ndi chofunikira kwambiri. Ndipo choona chakuti amalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pa nthawi yomweyi ndiye chofunika ngakhale kwambiri. Sitimalalikira kokha uthenga wabwino kwa anthu a kudziko, koma kupitanso patsogolo ndi kuwatsogolera kuti alandire Mzimu Woyera panthawi yomweyi.
Tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu mu nthawi ino kwa iwo amene akufuna uwo, Kukanakhala kuti tinafuna kusiya kulalikira uthenga wabwino, tanthauzo lonse la ntchito zathu likanasowa. Tiyenera kukhala odziwa kuti uthenga wabwino umenewu umatsogolera anthu kuti akhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Pamene tikulalikira uthenga wabwino poganizira zimenezi m’maganizo, malawi a Mzimu Woyera adzafalikira ngati moto wolusa padziko lonse lapansi.
Pamene mlaliki wakhulupilira kuti uthenga wabwino ungatsogolere anthu adziko kuti alandire Mzimu Woyera, amafika podziwa mwamphamvu kuti utumiki wake siwakukopa anthu kuti akhulupilire mwa Yesu Kristu, koma ndi wakuthandiza iwo kuti alandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Motero, ndikofunika kwambiri kwa ife kuti tilalikire uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu pa nthawi ino.
Munthu amafunika kumvetsera ndi makutu ake ndi kukhulupilira ndi mtima wake mu uthenga wabwino umene timalalikira kuti alandire Mzimu Woyera. Momveka bwino, uthenga wabwino umene timalalikira uli ndi chikoka chachikulu pa miyoyo ya anthu. Mphamvu ya uthenga wabwino ndi ulamuliro ndiponso madalitso opatsidwa ndi Mulungu.
Petro anali mlaliki wa Ayuda, pamene Paulo anali wa iwo amitundu ina. Pamene Petro anali kupemphera pamwamba pa nyumba, anaona Kumwamba kutatseguka ndipo chinthu monga pepala lalikulu lomangidwa m’ngondya zinai likutsikira pa iye. M’kati mwake munali mitundu yonse ya nyama zodetsedwa zimene Baibulo linanena kuti zinali zoletsedwa kudya.
Petro anali asanadyepo chinthu wamba kapena chodetsedwa. Komabe, Mulungu anamulamula kuti aphe ndi kudya izo. Petro anakana, kunena kuti, “Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m’kamwa mwanga ndi kale lonse.” Ndipo mawu ananena naye kuti, “Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.” Kodi chimenechi chikuonetsa chiani? Mulungu akunena kuti Yesu anatsuka machimo onse adziko, ngakhale a anthu amitundu ina, pamene anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda.
Tanthauzo lauzimu la lamulo la Mulungu kuti iye aphe ndi kudya nyama zodetsedwa linali kuphunzitsa Petro kuti ngakhale anthu amitundu ina angakhale ana a Mulungu pokhulupilira kuti Yesu anatumizidwa padziko lino, anabatizidwa kuti achotse machimo athu onse ndi kupachikidwa kuti aweruzidwe m’malo mwawo.
Petro anali kutsatirabe ndondomeko ya lamulo m’malo moona ndi maso auzimu a chikhulupiliro, ngakhale pamene analandira Mzimu. Koma Petro analapa ndi kukhulupilira kuti Mulungu anatsuka kale ngakhale machimo a anthu amitundu ina. Petro anazindikira chuma cha uthenga wabwino okoma mwa kuya kwambiri. Iye anaona Mzimu Woyera ukugwera pa omvetsera ake pamene analalikira mawu a Mulungu.
Kodi tingasiyanitse bwanji ngati atumiki a lero alandira Mzimu Woyera kapena ai? Zikudalira ngati avomereza uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Munthu amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma monga m’mene ulili pamene mlaliki akulalikira mawu a Mulungu amalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Mzimu Woyera umene umakhala mu mtima mwa mlaliki nawonso umakhala mwa iye. Mlaliki ndi omvetsera adzakhala wogwirizana wina ndi mzake monga abwenzi a paunyamata. Iwo adzaona chikondi cha Mulungu chikukhala mwa wina ndi mnzake. Mlaliki adzaona omvetsera akukhala m’modzi wa anthu a Mulungu povomera uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Pamene tikulalikira uthenga wabwino, tingaone Mzimu Woyera ukutsika pa okhulupilira pamene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Si kaonedwe kosiyana ndi chipulumutso. Ndi chifukwa choyambirira chimene tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Uthenga wabwino umene tikulalikira ndi umene ukutengera ena kukalandira Mzimu Woyera.
Iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi ana a Mulungu. Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu sichiphunzitso cha zaumulungu cha chipembezo, ndipo motero pamene tikulalikira chimenechi kwa ena, amakhala ndi chikhulupiliro, kulandira Mzimu Woyera ndi kukhala ana a Mulungu. Kodi ndi dalitso lalikulu chotani limeneli! Kodi ndi odabwitsa chotani uthenga wabwino! Ndiponso ntchito Yake ndi yodabwitsa chotani! Iwo amene amalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu amathandiza kumanga Ufumu wa Mulungu. Timangolalikira uthenga wabwino, koma timalandira Mzimu Woyera.
Anthu ena amaganiza kuti kukhulupilira mwa Yesu ndi chinthu china ndipo kulandira Mzimu Woyera ndi chinanso. Motero, Akristu akupemphererabe Mzimu Woyera. Koma, Baibulo limanena kuti Mzimu Woyera umabwera pa iwo pamene akumvetsera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino olalikidwa ndi atumiki Ake. Anthu kuzungulira dziko lonse lapansi akufuna Mzimu Woyera. Uthenga wabwino umene timalalikira umawatsogolera iwo kuti akwaniritse khumbo lawo. Ndi chifukwa chake tiri ndi udindo wofalitsa uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Ndife ana a Atate ndi alowa m’malo Ake, amene ali okhulupirika ku Malipiro Ake a Pamwamba.
Tiyenera kulalikira uthenga wabwino ndi chikhulupiliro pamene tikusunga m’maganizo mwathu kuti cholinga chathu ndi kulola anthu kulandira Mzimu Woyera. Uthenga wabwino wa madzi ndi mzimu ndi chinthu chimene alaliki ayenera kukhulupilira moona asanalalikire kwa ena. Kenako omvetsera awo adzalandira mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino. Mwanjira imeneyi tingapumire moyo wosatha mwa iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino. Cholinga chathu ndi kuwapangitsa iwo kuti aomboledwe ku mphamvu ya mdima ndi kutembenuza iwo ku Ufumu wa Mulungu. Alaliki amasamutsa ochimwa oyenera kufa pansi pa mphamvu ya mdima kupita nawo mu Ufumu wa Mwana wa Mulungu. Ndi ntchito yofunika kwambiri yosintha ochimwa kukhala ana a Mulungu.
Anthu ambiri samadziwa mafungulo a kulandirira Mzimu Woyera ndipo amayesa kulandira Iye mwa mphamvu zawo. Komabe, izi zizatsimikiza kukhala zachabe. Chikhulupiliro chokha mu uthenga wabwino ndi chimene chikufunika, popeza chikhulupiliro chimamasula munthu ku machimo ake onse.
Kodi munalandira motani Mzimu Woyera? Kudzera mu pemphero? Kapena mwina kudzera mu kuika manja? Ai, iyo sindiye njira. Timalandira Mzimu Woyera pokhapo ngati takhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tiyenera kupemphera ndi kulalikira uthenga wabwino kotero kuti anthu onse a dziko alandire Mzimu Woyera.
Mawu akuti “mtumwi” akutanthauza “iye amene anatumidwa ndi Mulungu.” Kodi atumwi amachita chiani? Iwo amalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti anthu alandire Mzimu Woyera. Kodi simukufuna kutenga ntchito imeneyi pamodzi ndi ife? Tonse tiyenera kukhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi kulalikira uwo kwa anthu onse. Aleluya! Thokozani choonadi chonse cha uthenga wabwino umene Ambuye anatipatsa kuti tilandire Mzimu Woyera!