Search

FREE PRINTED BOOKS,
eBOOKS AND AUDIOBOOKS

The Gospel of the Water and the Spirit

KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA? [Kusindikiza Kokonzedwanso Kwatsopano]
  • ISBN9788928261703
  • Pages406

Chichewa 1

KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA? [Kusindikiza Kokonzedwanso Kwatsopano]

Rev. Paul C. Jong

ZAM’KATIMU
 
Chigawo Choyamba — Maulaliki 
1. Choyamba Ife Tiyenera Kudziwa Machimo Athu kuti Tiomboledwe (Marko 7:8-9, 20-23) — 21
2. Anthu Amabadwa Wochimwa (Marko 7:20-23) — 41
3. Ngati Ife Tichita Zinthu Motsatira Lamulo, Kodi Ilo Lingatipulutse Ife? (Luka 10:25-30) — 55 
4. Chiombolo cha Muyaya (Yohane 8:1-12) — 79 
5. Ubatizo wa Yesu ndi Chitetezero cha Machimo (Mateyu 3:13-17) — 115
6. Yesu Kristu Adadza mwa Madzi, Mwazi, ndi Mzimu Woyera (1 Yohane 5:1-12) — 171 
7. Ubatizo wa Yesu Ndi Chifaniziro cha Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22) — 211 
8. Uthenga Wabwino wa Chiombolo Chochuluka (Yohane 13:1-17) — 233 
 
Chigawo Chachiwiri — Mau Owonjezera
1. Umboni wa Chipulumutso — 307 
2. Kufotokoza Kowonjezera — 329
3. Mafunso ndi Mayankho — 367
 
 
Mutu waukulu wa bukuli ndi "kubadwa mwatsopano mwa Madzi ndi Mzimu Woyera." Ili ndi chiyambi chake pa mutuwu. Mwanjira ina, bukuli limatiwuza momveka bwino chomwe kubadwa mwatsopano kuli ndi mmene tingabadwire mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera molingana ndi Baibulo. Madzi amaimira ubatizo wa Yesu ku Yordano ndipo Baibulo limati machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Yohane anali woimira anthu onse ndiponso mdzukulu wa Aroni, Wansembe Wamkulu. Aroni anasanjika manja ake pamutu pa mbuzi yopereka nsembe ndipo anapititsira machimo onse a chaka cha Aisraeli pa iyo pa Tsiku la Chiyanjanitso. Ichi ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zikubwera. Ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha kusanjika manja. Yesu anabatizidwa m`njira ya kusanjika manja ku Yordano. Choncho Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera mu ubatizo Wake ndipo anapachikidwa kuti alipire machimowo. Koma Akhristu ambiri sadziwa chifukwa chake Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu Yordano. Ubatizo wa Yesu ndi mawu ofunika kwambiri a bukuli ndiponso gawo losatheka kuchotsa la Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera. Tikhoza kubadwa mwatsopano pokhapokha titakhulupirira mu ubatizo wa Yesu ndi Mtanda Wake.
eBook Download
PDF EPUB
AudioBook
AudioBook

Book Reviews from Readers

  • NDINALI OCHIMWA KOMA TSOPANO NDINE MWANA WA MULUNGU OPANDA UCHIMO POKHULUPILIRA MU UTHENGA WABWINO WA MADZI, MWAZI NDI MZIMU.
    Brenda Tembo, Zambia

    OH INDE! NDINALI OCHIMWA KOMA TSOPANO NDINE MWANA WA MULUNGU OPANDA UCHIMO POKHULUPILIRA MU UTHENGA WABWINO WA MADZI, MWAZI NDI MZIMU
    Ndikuthokoza Mulungu posindikiza buku lapadera lotchedwa KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU? Kudzera mwa mtumiki Wake REV PAUL C.JONG.
    Kudzera mu kuwerenga buku limeneli, KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU? la REV PAUL C. JONG, ndamvetsetsa motheratu kuti ndinedi ndani monga munthu kupatula Yesu Kristu. Kuti ndinabadwa wa uchimo kwambiri, ndipo ndinaikidwira ku gahena zonse chifukwa cha machimo anga. Koma mathokozo akhale kwa Mwana Obadwa Yekha wa Mulungu, Yesu Kristu amene anadza ku dziko lino lapansi kusandulika m’thupi la munthu, ndipo pa zaka za 30 kupita ku Mtsinje wa Yordano kukakumana ndi Yohane Mbatizi amene anaimilira monga woimirira wa mtundu wa anthu komanso mkulu wa nsembe wotsiriza pa dziko lapansi pamene Iye anabatiza Yesu Kristu kuti apereke machimo anga onse otengera, akale, atsopano ndi a mtsogolo pa thupi la Yesu Kristu kudzera mu njira ya kuika kwa manja monga yodzodzedwa ndi Mulungu Atate M`chipangano Chakale mu (Levitiko 1:1-4, 16 ndime ya 21) yomwe imafanana ndi ubatizo wa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi mu (Mateyu 3:13-17). Chifukwa chakuti tsopano ndimakhulupilira mu Choonadi chimenechi kuti Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti atenge machimo anga onse komanso machimo a aliyense padziko lapansi ndi kupita pa mtanda kuti alipire mphotho ya machimo anga, ndipo pa tsiku lachitatu kuukitsidwa kuti apereke moyo watsopano, ndakhala tsopano mwana wa Mulungu wopanda uchimo komanso olungama. Aleluya!! Ulemelero wonse ndi Ulemu ziperekedwe kwa Yesu Kristu.
    Ndikupereka mathokozo anga kwa Mtumiki woona wa Mulungu, Rev. Paul C. Jong, pondidalitsa ine komanso dziko lonse lapansi ndi buku lapadera limeneli lokhala ndi mau enieni a chipulumutso omwe tsopano andipatsa ine mwayi wolowa Kumwamba monga ulendo wanga. Amen.

    More
  • INU SIMUYENERA KUPITA PAMASO PA MULUNGU NDI ZOYEMBEKEZERA ZANU KUPATULA KUTI MUPULUMUTSIDWE KU MACHIMO ANU.
    Wogwira Nao Ntchito, Zambia

    Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu akupatseni inu chisomo ndi mtendere ngakhale pamene inu mwadza kudzaphunzira ndi kukhulupilira mu choonadi cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, Ame!
    Ndikupereka mathokozo anga kwa Mulungu chifukwa cha buku lililonse lauzimu lolembedwa ndi Rev. Paul C. Jong. Pakuti kudzera m’mabuku Ake, Mulungu wafotokoza chipulumutso chathu ku uchimo mu njira yophweka. Ulemelero ukhale kwa Mulungu.
    Lero anthu ambiri sadziwa Chipulumutso choona chimene Yesu Kristu wabweretsera mtundu wa anthu, ndipo izi zili choncho chifukwa chakuti anthu ambiri amakonda kubisa umunthu wao weniweni, ndipo m’malo mwake iwo amayesetsa mwakhama kufika kwa Mulungu ndi zokumva zao zathupi kuganizira za mtanda wa Yesu wokha, kuganiza kuti, O Ambuye wanga Yesu munandifera ine, pepani, chonde ndikhululukireni, sindidzachimwanso, inde Ambuye ndikulonjeza kuti sindidzachimwanso. Zimene ndi zoipa kwambiri! Pamene anthu amenewo kwenikweni akudziletsa okha kukumana ndi Mulungu woona amene anadza ndi Uthenga Wabwino wa choonadi wa Madzi, Mwazi ndi Mzimu. Choncho, ndikukudandaulirani inu kuti mudziwe kuti kulira kwambiri chifukwa cha kukhetsa mwazi kwa Yesu, kutengeka mtima ndi nyimbo za uthenga wabwino zosakwanira ndi kupereka tsiku lililonse mapemphero akulapa komanso kuyesa kuchita ntchito zabwino, sizingakutsogolereni inu kuti mukumane ndi Mulungu m’modzi yekha woona amene anadza ndi Uthenga Wabwino wa choonadi wa madzi ndi Mzimu(Yohane 3:5).
    Koma, mwamwayi wokwanira inu mudakali ndi mwayi wobwerera kuchokera ku kudzinyenga nokha ngati inu mungadzichepetse chabe nokha podziwa moona mtima khalidwe lanu lenileni la uchimo(Marko 7: 21-23) ndi kuvomera kuti ndinu ndani mapaso panu ndi pamaso pa Mulungu. Motero pochita choncho, ndi mitima yodzichepetsa, kenako Mulungu woona adzakupatsani inu Uthenga Wabwino wa choonadi wa madzi ndi Mzimu umene uli ndi ubatizo wa Yesu wochokera kwa Yohane (kumene Iye anatsuka machimo a dziko lapansi), imfa Yake pa Mtanda (pamene Iye analipira mphotho yonse ya uchimo) ndi Mzimu (amene Iye anaukira kuti apereke Moyo Watsopano kwa aliyense amene amakhulupilira). Kuyambira pamenepo, pokhulupilira mu Uthenga Wabwino woona umenewu wa madzi ndi Mzimu, machimo a mu mtima mwanu adzasowa motheratu ndipo inu kenako mudzapeza mwayi wokhala mwana wa Mulungu mulimonse, kuyamba kuyandikira kwa Iye ndi mtima woyera. Aleluya!
    Wogwira Nao Ntchito, Zambia

    More

Books related to this title