NDIKUPEREKA MATHOKOZO ANGA CHIFUKWA CHA UBATIZO WANU, IMFA KOMANSO KUUKA, KUDZERA MU BUKU1 LAPA INTANETI.
O Ambuye, O Ambuye, kodi dzina Lanu ndi lolemekezeka bwanji lomwe ndi loposa maina onse. Pakuti kudzera mu mphamvu ya dzina Lanu, Inu mwatipatsa ife moyo wopanda uchimo. Inde Ambuye kudzera mu mphamvu ya dzina Lanu lomwe limanyamula Machitidwe Anu olungama a ubatizo Wanu omwe Inu mudalandira kuchokera kwa Yohane Mbatizi kuti mutenge Machimo onse adziko lapansi, ndipo ndi mwazi Wanu wamtengo wapatali omwe Inu munakhetsa pa mtanda Inu munalipira mphotho ya machimo athu, komanso ndi kuuka Kwanu kumene ife tapezera moyo watsopano, moyo wopanda uchimo. O Ambuye Mulungu wathu, kodi ndife ndani kuti tikane mau anu, ndife chabe zolengedwa Zanu Atate, amene tikufunika kokha kuvomereza khalidwe lathu pamaso Panu. Kodi ndife ndani monga munthu? Ndife obadwa ochimwa ndi mitundu yathu 12 ya machimo okhazikika m’mitima mwathu komanso ndi malingaliro olakwika, ndipo chifukwa cha chimenechi ulendo wathu siwina koma opita ku gahena popanda zotsutsa zilizonse. O Ambuye, ngati Inu mutiitana ife ochimwa ndiye kuti ndithudi ndife ochimwa, ndipo ngati inu mutiitana ife olungama, ndiye kuti ndithudi ndife olungama. Motero ndi mau Anu a Lamulo, ndikuvomereza kuti ndine obadwa ochimwa, monga ndinatengera uchimo kuchokera kwa makolo anga Adamu ndi Hava. Koma tsopano O Ambuye, ndikuvomereza molimba mtima kuti ndine olungama, inde O Ambuye ndine olungama osati chifukwa sindinachite uchimo, kapena ndapereka chinachake cha ine ndekha kuti ndikhale opanda uchimo, Ai! Ndine olungama chifukwa chakuti ndazidziwa ndekha kubadwa ochimwa pamaso Panu O Ambuye, ndipo chifukwa cha chimenechi, Inu mwavumbulutsa njira imodzi komanso yokhayo yomwe ine ndapulumukira ku machimo anga onse. Inu mwandipulutsa ine ndi ubatizo Wanu umene Inu munalandira kuchokera kwa Yohane Mbatizi, Mkulu Wansembe wotsiriza padziko lapansi komanso woimirira wa ife tonse mtundu wa anthu amene ndi obadwa ochimwa, iye anapereka machimo athu pa thupi lanu lolungama monga Mkulu Wansembe wotsiriza ndipo Inu modzichepetsa mudalandira iwo O Ambuye, kenako Inu mudakhala ndi uchimo chifukwa cha ife, Inu amene simunadziwe uchimo uliwonse. Machimo anga amene Inu mudalandira pa ubatizo Wanu kuchokera kwa Yohane Mbatizi, anakupangitsani Inu kuvutika mwankhanza pa Mtanda, kulipira mphotho ya machimo anga pokhetsa kwa mwazi Wanu wamtengo wapatali kuti mundipatse ine chikhululukiro chonse cha machimo anga monga Yohane 19:30 amatsimikizira icho chonse. Kenako Inu munaukanso kuti mundipatse ine moyo watsopano mwa Inu, ndiye kuti moyo wopanda uchimo uliwonse konse, osati ngakhale banga la uchimo latsala mu mtima mwanga. Pakuti Inu munasesa uwo onse ndi ubatizo Wanu, imfa ndi kuuka Kwanu. Motero ndikukuthokozani Inu Ambuye, chifukwa cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu pa moyo wanga. Amen.