" Kow padha olh tanpa nganggo mbayar gunakna tanpa nganggo bayaran " (Matius 10:8)

HOME  |  PETA SITE  |  KONTAK  |  PERTOLONGAN    
Pelajaran Alkitab Buku Kristen Gratis eBook Kristen Gratis Tentang Kami
  E-book gratis dalam bahasa Chichewa edisi 21

 


Kugwirizana Pakati pa Utumiki wa YESU ndi uja wa YOHANE M'BATIZI Wolembedwa mu Mauthenga Anai

 • Format e-book : Acrobat PDF Reader
 • Download sampai sekarang : 12
 • Mengenai Buku ini
 • Daftar isi
 

Kulengeza:

Bukuli limalankhula kwa Ife Molimbika Kwambiri za Kufunikira kwa Utumiki wa Yohane M'batizi

Kufothokoza:

Pangano Latsopano liyamba ndi Mauthenga Anai, aya ndi, Uthenga wa Mateyo, Marko, Luka, ndi wa Yohane. Mauthenga onse Anai amachita ndi kulemba mokwana za utumiki wa Yohane M'batizi. Ndi cifukwa chakuti utumiki wake ndi wofunikira kwambiri. Kopanda kumvetsa utumiki wa Yohane M'batizi, sitinganene kuti tidziwa utumiki wa Yesu Khristu. Mauthenga wofunikira kwambiri kotero?" Kulosera za Yohane M'batizi, ngakhale Yesu anati, "Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndiye 'Eliya woyembekezeka kubwera uja" (Mateyo 11:14).Choncho, Yohane M'batizi anali munthu obadwa padzikoli lapansi kuti achite utumiki wopatulika. Yesu ananenanso, "Kuyambira m'matsiku a Yohane M'batizi m'paka tsopano ufumu wa kumwamba ndi wokangamizidwa, ndipo wokangamirawo amaukwatula mwa mphamvu" (Mateyo 11:12). Ichi ndi choonadi cifukwa Yohane M'batizi anabadwa padzikoli lapansi, ndipo pamene anabatiza Yesu Khristu, machimo adzikoli lapansi anaperekedwa pa Iye. Ndimmene Yesu anakwanilitsira kutenga machimo ya dzikoli lapansi mwa kamodzi. Pomvomereza kuti ichi chikhale tero, Ambuye anamvomereza onse amene anakhulupilira mu utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumikiwa Yesu kuti alowe Kumwamba polandira kutsukidwa kwa machimo. Ili ndi tanthauzo la Malemba ya mndime yo chokera mu Uthenga wa Mateyo chapitala 11, ndime ya 12-14.
Kodi mukhulupilira kuti Uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi Choonadi? Ngati mukhulupilkira, chitanthauza kuti mkuudziwa utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu mofikapo. Koma, Akiristu ambiri amene samvesetsa utumiki wa Yohane M'batizi sakudziwa Choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndipo akhala umoyo wao wa chikhulupiliro mu zofuna zokha za mathupi awo. Ngakhale muumbuli, anthu otero safuna ngakhale kudziwa za utumiki wa Yohane M'batizi wolembedwa mu Mauthenga Anai. Koma, utumiki wa Yohane M'batizi wakhala nthawi itali pakusulidwa ngakhale pakati pa Akiristu amene akunena kuti akhulupilira. Mwina pa cifukwa ichi, Ndipeza kuti si anthu ambiri amene ali ndi chidwi mu utumiki wa Yohane M'batizi matsiku ano. Ndimmene, anthu amaona chachilendo ku onse amene ali ndi chidwi pa mutu uyu. Ndi cifukwa chakuti anthu ambiri akhala akuyangana pa utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu mosayikako nzeru kwa nthawi yaitali.

Mau a wosindikiza:

Poyamba tiyenera kudzindikira kuti Yesu ndi wa nchito wa utumiki amene anakwanilitsa chilungamo chonse cha Mulungu polandira ubatizo kwa Yohane M'batizi monga mowe zanenedwa mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Akiristu onse okhala mtsiku ili ndi nthawi iyi ayenera kudziwa wonse utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu. Tsopano tiyenera kubwerera ku Mau a Yehova, ndi pamene tiyenera kuganizira pa cifukwa cimene kuyenera kukhalira utumiki wa Yohane M'batizi ndi kukhulupilira mu iwo. Tsopano tiyenera kulowa mu utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu, ndiponso tiyenera kukonzanso chikhulupiliro chathu mofikapo. Tikachita tero, onse amene akhala padzikoli lapansi ayenera kuyembekezera kubera ku tsiku pamene onse adzadzindikira chilungamo cha Mulungu. Chikhulupiliro chotero ndi kumverera chifuniro cha Mulungu amene ndi woyenera.


 
Free Christian eBooks
    Daftar e-book
    Edisi bahasa Chichewa 21
 
 • Mengenai Buku ini
 •  
 • Daftar isi
 •     Apakah e-book
   
 • Mengenai e-book
 •  
 • Bagaimana membaca e-book
 •  
 • Pertanyaan yang paling sering ditanyakan
 •  
 • Pertolongan untuk Download
 •     Software pembaca e-book
   
 • MS Reader 2.0
 •  
 • Acrobat Reader 4.0
 •  

     
  Copyright © 2001 - 2019 The New Life Mission. ALL RIGHTS reserved.