ZAM’KATIMU
Chigawo Choyamba — Maulaliki
1. Choyamba Ife Tiyenera Kudziwa Machimo Athu kuti Tiomboledwe (Marko 7:8-9, 20-23)
2. Anthu Amabadwa Wochimwa (Marko 7:20-23)
3. Ngati Ife Tichita Zinthu Motsatira Lamulo, Kodi Ilo Lingatipulutse Ife? (Luka 10:25-30)
4. Chiombolo cha Muyaya (Yohane 8:1-12)
5. Ubatizo wa Yesu ndi Chitetezero cha Machimo (Mateyu 3:13-17)
6. Yesu Kristu Adadza mwa Madzi, Mwazi, ndi Mzimu Woyera (1 Yohane 5:1-12)
7. Ubatizo wa Yesu Ndi Chifaniziro cha Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22)
8. Uthenga Wabwino wa Chiombolo Chochuluka (Yohane 13:1-17)
Chigawo Chachiwiri — Mau Owonjezera
1. Kufotokoza Kowonjezera
2. Mafunso ndi Mayankho
(Chichewa)
Mutu waukulu wa bukuli ndi "kubadwa mwatsopano mwa Madzi ndi Mzimu Woyera." Ili ndi chiyambi chake pa mutuwu. Mwanjira ina, bukuli limatiwuza momveka bwino chomwe kubadwa mwatsopano kuli ndi mmene tingabadwire mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera molingana ndi Baibulo. Madzi amaimira ubatizo wa Yesu ku Yordano ndipo Baibulo limati machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Yohane anali woimira anthu onse ndiponso mdzukulu wa Aroni, Wansembe Wamkulu. Aroni anasanjika manja ake pamutu pa mbuzi yopereka nsembe ndipo anapititsira machimo onse a chaka cha Aisraeli pa iyo pa Tsiku la Chiyanjanitso. Ichi ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zikubwera. Ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha kusanjika manja. Yesu anabatizidwa m`njira ya kusanjika manja ku Yordano. Choncho Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera mu ubatizo Wake ndipo anapachikidwa kuti alipire machimowo. Koma Akhristu ambiri sadziwa chifukwa chake Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu Yordano. Ubatizo wa Yesu ndi mawu ofunika kwambiri a bukuli ndiponso gawo losatheka kuchotsa la Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera. Tikhoza kubadwa mwatsopano pokhapokha titakhulupirira mu ubatizo wa Yesu ndi Mtanda Wake.
(Italian)
Il soggetto principale di questo titolo è "nato di nuovo dall`Acqua e dallo Spirito". C`è originalità nell`argomento. In altre parole, questo libro informa con chiarezza cosa significa essere nato di nuovo e come essere nato di nuovo dall`acqua e dallo Spirito in stretto accordo con la Bibbia. L`acqua simbolizza il battesimo di Gesù sul Giordano e la Bibbia dice che tutti i nostri peccati sono stati passati a Gesù quando fu battezzato da Giovanni Battista. Giovanni era il rappresentante di tutta l`umanità e un discendente di Aaronne, il Sommo Sacerdote. Aaronne posava le mani sulla testa del capro espiatorio e trasferiva tutti i peccati annuali degli Israeliti su di esso nel Giorno dell`Espiazione. È l`ombra delle cose buone a venire. Il battesimo di Gesù è l`antitipo della imposizione delle mani. Gesù fu battezzato nella forma dell`imposizione delle mani sul Giordano. Così ha tolto tutti i peccati del mondo attraverso il suo battesimo e fu crocifisso per pagare per i peccati. Ma la maggior parte dei cristiani non sa perché Gesù fu battezzato da Giovanni Battista sul Giordano. Il battesimo di Gesù è la parola chiave di questo libro e la parte indispensabile del Vangelo dell`Acqua e dello Spirito. Possiamo essere nati di nuovo solo credendo nel battesimo di Gesù e nella sua Croce.
Next
Chichewa 2: BWELERANI KU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU
Italian 2: RITORNO AL VANGELO DELL’ACQUA E DELLO SPIRITO