Cziczewa 2
Rev. Paul C. Jong
Pomimo tego, że pandemia Covid-19 już się zakończyła, nadal istnieją trudności w wysyłaniu pocztą lub otrzymywaniu naszych drukowanych książek z powodu różnych trudnych sytuacji międzynarodowych. Kiedy sytuacja międzynarodowa ulegnie poprawie i normalizacji, wznowimy wysyłkę drukowanych książek.
Ndisanakhulupilire mu uthenga wabwino wa Choonadi wa madzi ndi Mzimu (Yohane 3:5), ndinali kwenikweni Mkristu wochimwa, amene ndidakhulupilira mwa Yesu koma ndidali ndidakali ndi uchimo mumtima mwanga, ngakhale ndidakhulupirira m’mwazi wa Yesu mwakhama, ndidali ndidakali ndi uchimo mokhazikika mumtima mwanga. Kodi ndi chikhulupiliro chosokonezeka komanso chotsutsa bwanji chomwe ndidali nacho!
Koma pambuyo powerenga Buku la REV. PAUL C. JONG lotchedwa BWERERANI KU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU,
Ndakhulupilira mwa Yesu molondola, pamene buku limeneli BWERERANI KU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU, la Rev. Paul C. Jong tsopano lasandutsa chikhulupiriro changa kukhala chikhulupiriro cholondola komanso choyera m`Machitidwe olungama a Yesu Kristu omwe ndi njira Yake yokha yomwe Iye anatipulumutsira ife ku machimo athu onse, kapena machimo adziko lapansi monga Yohane anachitira umboni mu (Yohane 1:29) ngakhale, kudzera mu ubatizo Wake, imfa ndi kuuka zimene zalola mtima wanga kukhala opanda uchimo komanso oyera. Motero sindinenso Mkristu wochimwa, ngakhalenso wokhulupilira wachinyengo monga kale. Tsopano chikhulupiriro changa chabodza chokhulupilira mwa Yesu monga Mpulumutsi wanga koma kukhalabe ndi uchimo mumtima mwanga chasowa motheratu zonse chifukwa cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, omwe uli m’buku limeneli. Tsopano ndimakhalira kupereka mathokozo kwa Mulungu chifukwa cha Mtumiki Wake Rev. Paul C. Jong polemba buku lapadera lotero ngakhale, BWERERANI KU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU pakuti ilo landipangadi ine kusanduka kukhala mwana wa Mulungu wopanda uchimo, popanda mphamvu zanga, ntchito ngakhalenso mapemphero anga akulapa. Aleluya!
Tsopano ndamvetsetsa motheratu kuti UBATIZO WA YESU NDI MWAZI KUCHOTSERA UCHIMO MUMTIMA MWANGA ZIMAPANGA MTIMA OPANDA UCHIMO, MONGA MOMWE CHIMODZI KUCHOTSERA CHIMODZI INDEDI ZIMAPANGA PALIBE.
ALELUYA! MULUNGU ADALITSE NTCHITO YAKE YA CHILUNGAMO YA UBATIZO WAKE, IMFA NDI KUUKA.