Search

书评

NDI KUMVETSETSA KWA KALE KUTI NDALANDIRA KUMVETSETSA KWA TSOPANO.

  • Brenda Tembo
  • Zambia
  • 1493
  • 01/29/2024

 

  • ISBN
  • 页码
  • 評價

NDI KUMVETSETSA KWA KALE KUTI NDALANDIRA KUMVETSETSA KWA TSOPANO.
Ndikupereka mathokozo anga kwa Mulungu chifukwa cha chakudya chathu cha tsiku ndi tsiku kuchokera ku buku 5 lathu la uzimu la Rev. Paul C Jong, lotchedwa kuti AMBUYE WATHU YEMWE WAKHALA CHILUNGAMO CHA MULUNGU (I). Limene inu mungalipeze popita ku www.bjnewlife.org. Pambuyo powerenga buku limeneli, ndatsimikiza chikhulupiriro changa ngakhale kwambiri mu Machitidwe olungama a Ambuye wathu Yesu Kristu a ubatizo Wake, imfa ndi kuuka. Mu kupherezera, ndikupitiriza kupereka mathokozo anga kwa Ambuye pondilola ine kumvetsetsa chipulumutso changa, choyambilira pondilola ine kuti ndilandire chidziwitso cha chitetezero cha machimo cha Chipangano Chakale, kumene Mulungu anadzodza nyama ya nsembe kunyamula machimo machimo a anthu aku Israyeli kudzera mu kuika kwa manja kwa Mkulu Wansembe pa mutu pake kuti asamutsire machimo onse a anthu aku Israyeli pa mutu pake. Kenako nyama ya nsembe inkatha kuphedwa chifukwa cha machimo a Aisrayeli ndipo ndi mwazi wake iyo inkalandira chiweruzo m`malo mwao kuti awapatse iwo chikhululukiro cha machimo awo. Aleluya!
Mofanana, kudzera mu chidziwitso chimenechi cha Chipangano Chakale, Ambuye wandilola ine kuti ndilandire chidziwitso cha chitetezero cha machimo athu cha Chipangano Chatsopano, kuti Yesu Kristu Mwanawankhosa wa Mulungu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi Mkulu Wansembe wotsiriza padziko lapansi, kudzera kuika kwa manja ake a Yohane Mbatizi pa mutu wa Yesu Kristu, iye anasamutsira machimo anga onse komanso machimo adziko lapansi pa thupi la Yesu Kristu kamodzi kokha, tsopano monga thupi lolungama la Yesu Kristu linavomera machimo anga onse komanso machimo adziko lonse lapansi, Iye anaweruzidwa m`malo mwanga komanso m`malo mwa mtundu wonse wa anthu pokhetsa mwazi Wake wamtengo wapatali pa Mtanda. Ndipo kuukanso kwa akufa pa tsiku lachitatu kuti andipatse ine moyo watsopano, wodzala ndi Mzimu ndi Choonadi tsopano kuti ndimakhulupilira mu chikhulupiriro cha machimo anga. Motero tsopano ndili ndi chitsimikizo chotheratu cha chipulumutso changa kudzera mu chikhulupiriro changa mu chidziwitso cha chitetezero cha machimo cha Chipangano Chakale, kufikira ku chikhulupiriro changa mu chidziwitso cha chitetezero cha machimo cha Chipangano Chatsopano. Pamene mapangano awiri amenewa akugwirizana kwambiri ndi dongosolo la Mulungu la chipulumutso cha mtundu wa anthu. Aleluya. Mulungu adalitse ntchito Yake ya chipulumutso yopezeka mu uthenga wabwino wa Choonadi wa madzi ndi Mzimu yomwe yakhala ikulalikdwa ndi Mtumiki Wake woona Rev.Paul C Jong (www.bjnewlife.org).
Brenda Tembo, Zambia