Search

Avis sur les Livres

NDALANDIRA KUKHAZIKIKA KWA MZIMU WOYERA NDI MPHAMVU YA UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU

  • Brenda Tembo
  • Zambia
  • 1494
  • 01/15/2024

English 3

HOW CAN WE RECEIVE THE HOLY SPIRIT AS A GIFT? [New Revised Edition]

Rev. Paul C. Jong

  • ISBN9788928261987
  • Pages463
  • Évaluation

NDALANDIRA KUKHAZIKIKA KWA MZIMU WOYERA NDI MPHAMVU YA UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU
Ndisanawerenge Mabuku a Rev. Paul C Jong, ndinali ndi uchimo mumtima mwanga ndipo Mzimu wa Mulungu sanali ndi ine zonse chifukwa cha machimo anga. Koma pambuyo powerenga Mabuku a Paul C Jong amene mungawapeze popita pa www.bjnewlife.org, ndakhulupilira mwa Yesu moonadi popanda kusankha kwachiwiri. Motero mwa chikhulupiriro changa mu ubatizo wa Yesu, imfa ndi kuuka, ndalandira Mzimu Woyera mumtima mwanga ndipo tsopano machimo anga onse asowa motheratu. Ndipo pokhulupilira mu uthenga wabwino wokongola umenewu wa madzi ndi Mzimu, ndaphunzira kuti zonse zimene anthu amaganiza zokhudza kulandira Mzimu kudzera mu kuika kwa manja kudzera mwa abusa awo, kulankhula m’malilime komanso kupemphera modzipereka zonse ndi bodza. Chifukwa chakuti pali njira imodzi yokha imene wina angalandilire Mzimu Woyera ndipo iyi si ina koma pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa Choonadi wa madzi ndi Mzimu. Ndi pokhulupilira mu Uthenga Wabwino umenewu kuti ife timayandikira pafupi ndi Mulungu, pakuti Uthenga Wabwino umenewu umachotsa uchimo onse m’mitima yathu, ndipo Mzimu wa Mulungu amadza kudzakhala mumtima WOPANDA UCHIMO, icho ndi chifukwa chake Yesu Kristu wapanga kukhala chotheka kupanga machimo onse adziko lapansi kusowa kudzera mu ubatizo Wake umene analandira kuchokera kwa Yohane Mbatizi ndipo chifukwa cha chimenechi, kwa ife amene amene takhulupilira mu ubatizo Wake Iye watilola ife kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kamodzi kokha monga kubadwanso kwathu ndipo ndi mwazi Wake wa pa Mtanda, ife talandira chikhululukiro chamuyaya cha machimo. Aleluya! Zikomo Mulungu pakuti ndamvetsetsa ngakhale kwambiri zokhudza kukhazikika kwa Mzimu Woyera powerenga Buku 3 la Rev. Paul C Jong, lotchedwa kuti NJIRA YA WABWINO KWA INU KUTI MULANDIRE MZIMU WOYERA. Pakuti ilo limasonyeza mokwanira molandilira Mzimu Woyera ndi zipatso zake. Ndikupereka mathokozo anga onse kwa Mulungu chifukwa cha uthenga wabwino wa Choonadi wa madzi ndi Mzimu kudzera mwa Mtumiki Wake Rev. Paul C Jong. Mulungu apitirize kumudalitsa iye nthawi zonse ponditsogolera ine kwa Mulungu m`choonadi ndi mu Mzimu kudzera m`Mabuku ake (www.bjnewlife.org). Ame!
Brenda Tembo, Zambia