Zamkati
Mau Oyamba
1. Muyenera Kudziwa ndi Kukhulupilira Utumiki Wa Yohane M’batizi (Marko 1:1-2)
2. Yohane M’batizi Sanali Wolephera (Mateyu 11:1-14)
3. Yohane M’batizi, Amene Anabwera Mnjira ya Chilungamo (Mateyu 17:1-13)
4. Wonani pa Utumiki Wa Yohane M’batizi! (Luka1:17-23)
5. Tiyeni Tonse Mokondwera Tisangalale Mu Ulemelero Wa Mulungu (Yohane1:1-14)
6. Kodi Muyadziwa Mautumiki a Atumiki a Mulungu Awiri? (Yohane 1:30-36)
7. Kodi Cifukwa Nciani Yesu Anayenera Kubatizidwa? (Yohane 3:22-36)
8. Falisani Uthenga Woona Ndi Nchito ya Yesu Yolungama (Mateyu 3:1-17)
9. Kugwirizana Pakati pa Nchito ya Yohane M’batizi ndi Uthenga wa Kupepetsera Machimo Yathu (Mateyu 21:32)
10. Yesu Amene Anabwera Kuzafafaniza Machimo Yanu (Mateyu 3:13-17)
11. “Taona, Ine Ndikutumiza Mthenga Wanga” (Marko1:1-5)
12. Tiyene Tikhulupilire mwa Yesu mwa Kumvesetsa kwa Yohane M’batizi (Luke 1:1-17)
Pangano Latsopano liyamba ndi Mauthenga Anai, aya ndi, Uthenga wa Mateyo, Marko, Luka, ndi wa Yohane. Mauthenga onse Anai amachita ndi kulemba mokwana za utumiki wa Yohane M'batizi. Ndi cifukwa chakuti utumiki wake ndi wofunikira kwambiri. Kopanda kumvetsa utumiki wa Yohane M'batizi, sitinganene kuti tidziwa utumiki wa Yesu Khristu. Mauthenga wofunikira kwambiri kotero?" Kulosera za Yohane M'batizi, ngakhale Yesu anati, "Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndiye 'Eliya woyembekezeka kubwera uja" (Mateyo 11:14).Choncho, Yohane M'batizi anali munthu obadwa padzikoli lapansi kuti achite utumiki wopatulika. Yesu ananenanso, "Kuyambira m'matsiku a Yohane M'batizi m'paka tsopano ufumu wa kumwamba ndi wokangamizidwa, ndipo wokangamirawo amaukwatula mwa mphamvu" (Mateyo 11:12). Ichi ndi choonadi cifukwa Yohane M'batizi anabadwa padzikoli lapansi, ndipo pamene anabatiza Yesu Khristu, machimo adzikoli lapansi anaperekedwa pa Iye. Ndimmene Yesu anakwanilitsira kutenga machimo ya dzikoli lapansi mwa kamodzi. Pomvomereza kuti ichi chikhale tero, Ambuye anamvomereza onse amene anakhulupilira mu utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumikiwa Yesu kuti alowe Kumwamba polandira kutsukidwa kwa machimo. Ili ndi tanthauzo la Malemba ya mndime yo chokera mu Uthenga wa Mateyo chapitala 11, ndime ya 12-14.
Kodi mukhulupilira kuti Uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi Choonadi? Ngati mukhulupilkira, chitanthauza kuti mkuudziwa utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu mofikapo. Koma, Akiristu ambiri amene samvesetsa utumiki wa Yohane M'batizi sakudziwa Choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndipo akhala umoyo wao wa chikhulupiliro mu zofuna zokha za mathupi awo. Ngakhale muumbuli, anthu otero safuna ngakhale kudziwa za utumiki wa Yohane M'batizi wolembedwa mu Mauthenga Anai. Koma, utumiki wa Yohane M'batizi wakhala nthawi itali pakusulidwa ngakhale pakati pa Akiristu amene akunena kuti akhulupilira. Mwina pa cifukwa ichi, Ndipeza kuti si anthu ambiri amene ali ndi chidwi mu utumiki wa Yohane M'batizi matsiku ano. Ndimmene, anthu amaona chachilendo ku onse amene ali ndi chidwi pa mutu uyu. Ndi cifukwa chakuti anthu ambiri akhala akuyangana pa utumiki wa Yohane M'batizi ndi utumiki wa Yesu mosayikako nzeru kwa nthawi yaitali.
ھور